MACRA yalamula mawailesi omwe amanenelera mpira wakunja kuti azikhala ndi chilolezo.

Advertisement

Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) yalamula nyumba zowulutsa mawu zomwe zimanenerera mpira pomwe zikuonera m’makanena akunja kapena a m’dziko muno kuti zikuyenera kupereka umboni oti zili ndi chilolezo chochita izi pasanathe masiku asanu ndi awiri kuchokera pa 5 February chaka chino.

Malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa ndipo yasainidwa ndi mkulu wa bungweli a Daud Suleman, kuchita mchitidwewu mosatsata malamulo ndi mlandu.

Kalatayi yapitiliza kunena kuti nyumba zonse zowulutsa mawu zomwe zipezeke zikupitiliza kukopera kapena kuwulutsa zomwe nyumba zina za m’dziko muno komanso zakunja zikuchita pamene sizinaonetse umboni ofunikawu zizapatsidwa chilango.

Bungwe la MACRA latchula nyumba zofalitsa nkhani monga Super Sport, Sky Sport, British Broadcasting Corporation (BBC), Deutsch Welle, Aljazeera ndi zina monga zitsanzo za nyumba zowulutsa mawu za maiko ena komwe nyumba zina zowulutsa mawu za m’dziko muno zikumatengako zinthu nkumaulutsa mopanda chilolezo.

Advertisement