Anamandwa olosela nyengo ati mwezi uno mvula ichepa kagwedwe kake

Advertisement
Heavy rains are expected to hit Malaiw

Akatswiri pa nkhani zolosela nyengo m’dziko muno ati a Malawi ayembekezere kulandila mvula yochepa mwezi uno wa February moyerekeza ndi mwezi watha.

Izi zanenedwa kudzera mu ulosi umene nthambi yoona za nyengo yatulutsa okhudza kagwede ka mvula mwezi uno.

Malingana ndi a zanyengo, madera ambiri dziko muno ayembekezere kulandira ng’amba yochuluka.

Ngakhale izi chili chomwechi, boma kudzera mu unduna wa za ulimi likulimbikitsa anthu ambiri amene akulandira ngongole za NEEF kuti ayambe ulimi wam’thirira ngati njira imodzi imeme ithandizire dziko lino kukhala ndi chakudya chokwanira.

Wolemba : Peter Mavu

Advertisement