Tibhebhetseni 10 pini – Blantyre Sinodi yapempha membala aliyese

Advertisement
CCAP BT Synod launches fundraising campaign to repay K2 billion loan

Pelekani molowa manja: Sinodi ya Blantyre pansi pa mpingo wa Church of Central Africa Presbyterian (CCAP) yakhazikitsa ntchito yobweza ngongole ya ndalama zokwana 2 biliyoni kwacha ndipo yagwada kupempha akhilisitu ake kupeleka 10,000 kwacha aliyese.

Sinodiyi Lamulungu pa 28 January, 2024, yatulutsa kalata yokhazikitsa ntchito yobweza ngongole ya ndalama zokwana 2 biliyoni kwacha yomwe mpingowu mbuyomu unalengeza kuti uli nawo.

Mwazina mu kalatayi yomwe yawelengedwa m’mipingo yose yomwe ili pansi pake, Sinodiyi yapempha ma membala ake kuti ayitchove Sinodiyi ndikanganyase kuti ikwanitse kubweza ngongole yomwe ili nayoyi.

Poti paja mwachaje satafuna, Sinodi ya Blantyre yati malingana ndi chiwerengero cha mamembala ake, ntchitoyi itha kugwilika bwino mosavuta ngati membala aliyese atapeleka ndalama yosachepela  10,000 kwacha.

Kupatula kalatayi, Sinodiyi inakhazikitsa ntchito yobweza ngongoleyi kudzera pa mwambo omwe unachitikira pa mpingo wa St. Michael and all Angels mu Presbytery ya Blantyre city komwe Moderator wa Sinodiyi, m’busa Dr Humphreys Zgambo analimbikitsa akhilisitu onse pansi pa sinodiyi kuti athandize mpingowu kubweza ngongole yomwe ilipoyi.

Advertisement