Mwana wafa ku Machinga atadya nsima ya gaga

Advertisement

Mwana  wa zaka zisanu ndi ziwiri wafa pomwe wina akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Machinga atadya nsima yomwe anaphikira gaga m’mudzi wa Makangata.

Mwana yemwe wamwalirayo dzina lake ndi Yamikani Witness wa m’mudzi wa mfumu yaikulu Nkoola.

Wapampando wachitukuko ku Makangata wauza nyumba zofalitsa nkhani kuti anthu asanu ndi m’modzi  anayamba kusanza komanso kutsekula m’mimba atadya nsimayi ndipo anawatengela ku chipatala.

Mneneri wachipatala cha Machinga a Wongani Nyirenda wati Witness anamwalira pa chipatala cha Machinga akulandira Thandizo pomwe ena awiri akupezako bwino.

Malingana ndi a Nyirenda, zotsatira zasonyeza kuti anthuwa anadya chakudya chomwe chinali cha poizoni.

Iwo anatinso mwana yemwe wamwalirayo komanso wina yemwe akulandira thandizo anawapeza ndi nthenda ya Malungo.

Advertisement