Mnyamata wagwililira mbuzi ku Ntchisi

Advertisement
Malawi24.com

Zina inu mkumafunsa kuti kodi anyamata oshanganipawa akukanika kufunsira mbeta? Zina ndithu ukamva ngati kutulo. Mnyamata wazaka 26 ku Ntchisi ali mchitokosi cha apolisi kamba koti amachita zadama ndi mbuzi.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Sub Inspector Salomy Zgambo, mnyamatayu dzina lake ndi Vincent Mwale ndipo adachita zamalawulozi la chinayi pa 25 January chaka chomwe chino.

Nkhani yonse ikuti patsiku lomwe mkuluyu amachita zadamazi ndi mbuziyi mwini wake anatutumuka atamva mbuzi yakeyo ikulira mwachilendo kwambili komanso modabwitsa zedi.

Apa mwini wakeyo adathamangira pa malo pomwe iye adayimangilira kuti izidya msipu koma mwini wakeyo adangoti kukamwa yasaa poona mnyamatayu akuchita zadama ndi mbuziyo.

Anthu ena tamva kuti mkuluyu amachita zadama ndi mbuziyo iwo anayankha kuti aka sikoyamba nyamatayu kuchita zadama ndi mbuzi ponena kuti wakhala akutero.

Vincent Mwale amachokera m’mudzi wa Magana kwa mfumu yayikulu Vuso Jere m’boma lomweri la Ntchisi.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement