Digili, kapena mteleshede? Dan Lu, Lombwe akusambulana uku

Advertisement

…Lombwe akuti nzakeyo anakhomera ku dowa

“Lu-Lo my vote”: Kuli kusambwadzana za mkabudula uku pomwe mtsutso wa ubwino wokhala ndi digili kapena kungokhala ndi chilembwe basi, wafika pa mwana wakana phala pakati pa oyimba Dan Lu ndi Kabol Lombwe ndipo nkhaniyi yatsikira ku ma Area.

Nkhaniyi inayamba pa 19 January, 2024 pomwe oyimba Dan Lufani analemba pa tsamba lake la fesibuku kuyitaniza anthu omutsata omwe iye amati ngakhale kuti alibe tsamba la digili, ndipo lilime lawo silinatambasuke kuti aziyankhula chizungu chothyakuka bwino, akukhala moyo wosangalala.

“Onse amene timanenedwa kuti ndife ma Savage mafana osatha kulankhula English koma timakhala moyo owaposa ama degree wo bwerani pano mafana aziwindi #2024MutinvaZigege,” anatelo Dan Lu pa tsamba lake la fesibuku.

Nkhaniyi inaveka monyung’unya kwa anthu angapo kuphatikizapo yemwe amathandiza oyimba, Kabol Lombwe yemwe naye analemba pa tsamba lake la fesibuku ndi kutsutsana ndi zomwe Dan Lu analankhulazo ponena kuti digili ndiyofunika kwambiri pa moyo wa munthu.

Lombwe yemwe pano amathandizira oyimba otchuka Nepman, wati ndizovetsa chisoni kuti Dan Lu azikayankhula musimbwa pa nkhani ya digili pomwe oyimbayu thupi lake likachita konya amapita ku chipatala komwe amakathandizidwa ndi akatswiri ama digili akuwanenawo.

“Zimakhala zomvesa chisoni ukamamva munthu wankulu akuti degree ndiyopanda ntchito simply because zake zimatheka opanda degree chonsecho akadwara amathamangila ku chipatala kuti akathandizidwe ndi munthu wa degree. Ati degree is just a paper mukadwara osamapita kwa nsing’anga bwanji,” anayankha Lomwe pa tsamba lake la fesibuku.

Chinkulirano chafika posauzana tsopano, ndipo awiriwa afika polozana dzala, kutchulana za mkabudula, mpaka Lombwe wafika pomuyalutsa Lufani kuti mwana wake oyamba uja siwake, ndipo akuti oyimbayu kalulu anamudutsa mphechepeche.

“Awuzeni anthu chilungamo, munatenga nkazi wa promoter wankulu ku USA atabwera kuzakupangani sign nkumusandusa nkazi wanu, awuzeni anthu kuti mwabanidwa pano simungapitenso ku America for 10 years coz munalandira ma 5 million kwa anthu kuti mupite nawo ku America ngati a band yanu asali oyimba (fraud).

“Auzeni anthu kuti mwana wanu uja bambo ake ndi anzanu aja inu simumabekeka, Mmawa mupangenso live ina. Don’t try me ndakupilirani ndatopa, ndikupasani zomwe mukufuna,” wateloso Lombwe mu uthenga omwe pakadali pano waufufuta pa tsamba lake la fesibuku.

Lombwe asanalembe izi pa tsamba lakeli, Dan Lu anachititsa nkumano wa anthu omutsatira p tsamba lake la fesibuku komwe anafotokoza zambiri za zomwe ankatanthauza pa zomwe analemba pa tsamba lake zokhudza kukhala ndi digili kapena ayi.

Iye wati uthenga omwe analembawu siunali ofuna kunyoza aliyese ndipo a kuti sanaganizile kuti anthu ena ngati Lombwe atha kudzamatuka ndikuyamba kumugenda miyala pa zomwe analembazo.

Advertisement