Mu 2024 mutimva Zigege — Watero Dan Lu


Oyimba Dan Lu watsindika kunena kuti chaka chino anthu amumva Zigege ndi nyimbo zimene akonze.

Dan Lu masiku ochepa apitawa adalemba pa tsamba lake la mchezo kuti “Onse amene timanenedwa kuti ndife ma Savage mafana osatha kulankhula English koma timakhala moyo owaposa ama degree wo bwerani pano mafana aziwindi #2024MutinvaZigege’

Izi zinazu)a mitima ya anthu ena makamaka amene ali ndi tsamba loyamba la sukulu ya ukachenjede (Degree) mpakana anthu ena adayikilapo ndemanga zofuna kubakira tsamba la ukachenjedeli.

“Ine monga oyimba cholinga changa chinali kulimbikitsa anthu amene alibe tsamba la sukulu ya ukachenjede (Degree) kuti apitilize kulimbikira posatengera kuti anthu ambiri amawayang’anira pansi koma sikuti ndimanyoza, chabe anthu anazimva molakwika,” Dan Lu.

Iye adapitiliza kunena kuti samayembekezera kuti anthu ena achilandira mwa mtundu umenewu komanso sikuti ndi njira imodzi yofuna kukopa anthu pofuna kutulutsa nyimbo yatsopano m’mene oyimba ena ama tsiku ano amachitira.

Mpungwepungwe pa tsamba la mchezo la fesibuku unapitlira pamene Kabolombwe yemwe amadziwika ndi nyimbo yomwe adayimba ndi Nepman yotchedwa Na Lero, adalemba zokhuza kubakira Degree tsiku lomwelo zimene zidamupangitsa Dan Lu kuganiza kuti amayinkhidwa zimene adanena pa tsamba lake.

“Kabolombwe ndilibe naye mulandu ndipo ndinakumana nayepo kamodzi Ku Studio Kwa Stich Fray Ku Blantyre sindimadziwa kuti ali nane zifukwa,” anatero Dan Lu.

Pakucheza kwathu, anauluranso kuti sabata loyamba la mwezi wa February atulutsa nyimbo yatsopano komanso kumapeto Kwa mwezi omwewo atulutsa chimbale chotchedwa ‘Mutimva Zigege’.

Kwa anthu onse amene amatsatira nyimbo zake adatsimikizira kuti nyimbo pafupifupi zisanu zilongosola mbiri yake kuti anthu adziwe kuti iyeyu ndi ndani kweni kweni komanso wadutsa muzotani.
Dan Lu adadziwika Koyamba mu chaka cha 2004 ndinyimbo yotchedwa Shupie.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.