Mbava za kapeti, tenti ya mtsogoleri wa dziko zagwidwa

Advertisement
Malawi presidential carpets

Agenda ku polisi chamba chili mthumba: Abambo awiri a m’boma la Mwanza athilidwa zingwe powaganizira kuti ndi omwe anakadawira galimoto ya boma ikuyenda ndikuba tenti komaso chinsalu chofiyira chija amayendapo mtsogoleri wa dziko m’misonkhano chija.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani za polisi mdziko muno a Peter Kalaya omwe kudzera mu kalata yomwe yatulutsidwa masana a lero Lachinayi, azindikira atsizina mtole awiriwa ngati a Lino Richard komaso a Jonasi Harlod omwe ndi a zaka 20 aliyese.

“Malawi Police Service (MPS) yamanga anthu awiri ndikupeza zinthu zonse zomwe zinabedwa mgalimoto ya unduna wa za mayendedwe ndi mtengatenga yomwe inaphulitsidwa m’mudzi mwa Laundi, m’mphepete mwa msewu wa Zalewa-Mwanza M6 pa ulendo wopita m’boma la Mwanza kukagwira ntchito zina,” yatelo mbali ina kalatayi.

Apolisi ati usiku wa Lachitatu pa 24 January, 2024 oganizilidwawa anakadamira galimoto ya ku nyumba ya chifumu yomwe inanyamula katundu yemwe amakasiyidwa ku Mwanza pokoNzekera msonkhano omwe a Lazarus Chakwera akuyenera kuchititsa Lachisanu m’bomali.

Richard komaso Harlod omwe ndiochokera m’mudzimwa Laundi Village, mfumu yaikulu Kanduku m’boma Mwanza, akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu wakuba.

Pakadali pano tenti ndi kapeti zomwe zapezekazi zikusungidwa ku polisi ya Mwanza podikilira kuti zizagwiritsidwe ntchito ngati umboni mlanduwu ukayambika

Advertisement