Katswiri pazamaphunziro wati phunziro la chingerezi lisamalepheretse ophunzira kupita ku yunivesite

Advertisement
Malawi University of Science and Technology Ranking

Poona kuti ophunzira ambili mdziko muno akulephera kupeza nawo mwayi ochita maphunziro msukulu za ukachenjede m’dziko lino kaamba ka chingerezi (English), yemwe ndi katswiri pankhani za maphunziro wapempha boma kuti lichotse chingerezi ngati phunziro limodzi lomuyenereza munthu kuti akachite maphunziro awukachenjede.

Katswiriyu yemwe dzina lake ndi a Ben Navitcha anati pali ophunzira ena amachita bwino kumaphunziro amasayansi koma kuchingereziku ndikumene kumakhala vuto kotero ophunzirawa amalephera kupeza nawo mwayi okachita maphunziro awukachenjede kamba kachingerezi.

Iye anapitilizanso kufotokoza kuti boma likuyenera kuwonjezeranso masukulu awukachenjede ndicholinga choti ophunzira ambili azitha kupeza nawo mwayi okachita maphunzirowa.

Pofuna kuti izi zitheke, iye anati kusintha masukulu osula a aphunzitsi (TTC) komanso sukulu zina za  sekondale kukhala za ukachenjede zitha kuthandizira kuti sukulu za ukachenjede mdziko lino zichuluke ndipo chiwerengero cha ophunzira omwe amasiyidwa kupeza nawo mwayiwu chitha kuchepa.

Padakali pano sukulu za ukachenjede za boma zimalola ophunzira yekhayo wakhoza chingerezi kupita ku sukuluzi.

Advertisement