Chepetsaniko zakazo ndimadwala nthenda ya shuga, inatero mfumu yogwilirayo

Advertisement

Mfumu ina yazaka 40 ku Lilongwe yalamulidwa kukaseweza jere kwa zaka 20 itapezeka yolakwa pa mlandu oti idagwilira mwana wazaka 13 m’munda wachimanga pamene mwanayo amkatchola nkhwani atatumidwa ndi amake.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Hastings Chigalu ati mfumuyi yomwe dzina lake ndi a Pitilosi Khote, adachita zadamazi ndi mwanayu m’mwezi wa June chaka chatha pamene mwanayu adatumidwa ndi amake kukatchola nkhwani m’munda.

Ndipo yemwe amayimira boma pa mlanduwu a Richard Kandeya anauza bwalo lamilanduli kuti mfumuyi idachita zadamazi ndi mwanayu cham’ma 6 m’mawa munthawi yomwe mwanayu amkatchola nkhwani.

Banja lina ndi lomwe ndilomwe lidapezerela mfumuyo ikuchita zamalodzazi ndi mwanayu koma mfumuyi idaopseza banjali ponena kuti banjalo lidamusokoneza zomwe amachitazo.

Bwalo la milanduli litafunsa za mulanduwu mfumuyo idayamba ndikukana mlanduwu ponena kuti adali asanalilire mwanayo.

Kenako mfumuyo inavomera mlanduwu ndikupempha bwalo la milanduli kuti limuchepetsere zakazo ponena kuti iye amadwala nthenda ya shuga koma bwalo lamilanduli silinamvere dandaulo lake mpaka walamulidwa kuti akaseweze ndende kwazaka 20 ndicholinga choti ena atengerepo phunziro.

Advertisement