DoDMA yalangiza maanja omwe akulandila chakudya kuti alimbikile ntchito zawo za tsiku ndi tsiku

Advertisement
Malawi maize distribution by DODMA

Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi m’dziko muno ya DoDMa yalangiza maanja amene akulandila chakudya kuchokera ku boma kudzera ku nthambiyi kuti apitilize kugwira ntchito zawo za tsiku ndi tsiku kuti akhale odzidalira pawokha.

Wanena izi ndi Mlembi Wamkulu ku Nthambiyi, a Charles Kalemba m’maboma a Karonga ndi Chitipa komwe amakhazikitsa ntchito yothandiza maanja omwe akusowa chakudya.

Kalemba wati anthuwa adzikhuthule kwathunthu kugwira ntchito m’minda ndi m’madimba osati manja lende.

“Ngati boma, tikuzindikira kuti munakhudzidwa ndi ngámba yoopsa chaka chatha. Nduna Yoona Za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi, Mtsogoleri wa Dziko lino Lazarus Chakwera, anabwera kudzakuyenderani. Tikudziwa kuti wanjala saangalowe m’munda. Pomwe mwadya, musakhale tambalale, limbikirani ntchito kuti inu ndi dziko lonse tikhale odzidalira. Nzomvetsa chisoni kuti ngati dziko tikupitilira kumavutika ndi njala pomwe tili ndi nyanja ndi mitsinje yochuluka,” anatero a Kalemba.

Ndipo mmawu awo, Mfumu Yaikulu Kilupula ya m’boma la Karonga anati bomali ndi lodalitsika ndi madzi ndipo ulimi wa nthilira ndiotheka, zikungofunika kuti anthu ayikepo chidwi.

Maanja 18,000 ndi omwe apindule ku Karonga ndipo m’boma la Chitipa, maanja 5778 ndi omwe alandire thandizo pansi pa ndondomekoyi.

Ntchito yi akuchitika pansi pa ndondomeko ya chaka cha 2023/24 (Lean Season Response) yomwe ikufikira anthu oposa 4.4 miliyoni m’maboma onse 28 komanso m’mizinda inayi ya m’dziko lino.

Advertisement