Katelele Ching’oma watisiya

Advertisement
Malawians musician Katelele Ching'oma

M’modzi mwa oyimba odziwika bwino kuno ku Malawi, Katelele Ching’oma, watisiya.

Oyimbayu wamwalira m’bandakucha wa lero ku chipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe komwe anamutengela.

Mchimwene wake wa oyimbayu, a Elvis Ching’oma, wati Katelele amadwala nthenda yokhudza chiwindi.

Moses Makawa, yemwe anali mnzake wa Katelele wati oyimbayu anagonekedwa ku chipatala masiku atatu apitawa.

“Amadwala inde koma masiku atatu apitawa ndi pomwe anagonekedwa pa Kamuzu Central kuchoka pachipatala cha Chinkhoma komwe anali. Lero ndi lomwe watisiya m’baleyu,” watero Makawa.

Katelele yemwe amakhala ku Dedza koma amachokela ku Nsanje wasiya mkazi ndi ana atatu, malingana ndi Makawa.

Oyimbayu anaimba nyimbo monga Waziputa wekha, Ndili nawo mwayi ndi Asowe zomwe zimakondedwa kwambiri.

M’bale wake Elvis wati nyimbo za Katelele zinapangitsa kuti banja la Ching’oma lidziwike chifukwa a Malawi ambiri amazikonda.

Advertisement