Sizachilendo kusintha dzina, watero katswiri wina

Advertisement

Kutsatira mpungwepungwe omwe wadza kamba koti a Lazarus Chakwera asintha dzina la chipatala cha Phalombe kukhala John Chilembwe Hospital, m’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo pa zochitika m’dziko muno a Wonderful Mkhutche ayankhula moyikira kumbuyo a Chakwera ponena kuti sizachilendo kusintha dzina.

Katswiriyu wayankhula izi pamene a Malawi ena akutsutsana ndi ganizo lomwe mtsogoleri wa dziko lino wachita ndipo mkunena kwawo akumati “Chakwera amange chipatala china mkuchitchula dzinalo.”

Apa a Mkhutche ayamikira ganizo la a Chakwera ponena kuti m’busa John Chilembwe adagwira ntchito yayikulu komanso yotamandika pomenyera ufulu wadziko lino ndipo anatinso sizachilendo mayina kusinthidwa popeza amatha kusinthidwa ndithu.

A Chakwera asintha dzinali ngati njira imodzi yosonyeza ulemu kwa John Chilembwe yemwe adagwira ntchito yomenyera ufulu wa dziko lino. Chipatalachi tsopano chizitchedwa kuti John Chilembwe Hospital.

Advertisement