Mbava zathyola ofesi ya Chilima ku Lilongwe

Advertisement
Vice President Saulos Chilima playing golf

Apolisi mu mzinda wa Lilongwe ati akusakasaka atsizinamtole omwe athyola ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ku Capital Hill ku Lilongwe momwe akuti abamo bisiketi ndi inki ya “printer”.

A Salome Zgambo omwe ndi ofalitsa nkhani ku polisi ya Lingadzi munzindawu, awuza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno kuti akuganizira kuti akathyaliwa apanga chipongwechi pakati pa lachisanu komanso usiku wa Lolemba pa 15 January, 2024.

Iwo ati pali chisonyezo choti akubawa anagwiritsa ntchito zenera la ku bafa kwa ofesi ya mlembi wa mkulu wa ofesiyi ndipo atalowa mkatimo, mbavazi zabamo “tonner” yemwe amagwiritsidwa ntchito posindikiza kalata zosiyana siyana komanso ma bisiketi.

Aka ndi kachiwiri kuti zoterezi zichitike kamba koti mzaka zitatu zapitazi, mu 2021, zoterezi zinachitikanso alonda angapo anamangidwa ndikuyimbidwa milandu ndipo ena mwa iwo akuseweza jele pano.

Advertisement