Chaponda walowa m’malo mwa Nankhumwa

Advertisement
George Chaponda

Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), chasankha a George Chaponda kukhala mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma m’nyumba ya malamulo, kulowa m’malo mwa a Kondwani Nankhumwa omwe adawachotsa m’chipanichi ndipo a tula pansi udindowu sabata latha.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe chipanichi chaatulutsa Lachiwiri pa 7 May, 2024 yomwe wasainira ndi Shadric Namalomba yemwe ndi oyankhulira chipanichi komaso mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika. 

Kupatula kusankhidwa kwa a Chaponda paudindowu, chipanichi kudzera chalengezanso za kusankhidwa kwa a Lonnie Chijere Chirwa ngati komishonala m’nyumba ya malamulo.

“Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndichokondwa kulengeza za kusankhidwa kwa a Hon George Thapatula Chaponda kukhala mtsogoleri watsopano wa zipani zotsutsa ku Nyumba ya Malamulo komanso Hon Lonnie Chijere Chirwa, MP ngati Commissioner ku Nyumba ya Malamulo,” yatelo kalata ya DPP.

Izi zikubwera patangodutsa maola ochepa pomwe Lolemba bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe, lachotsa chiletso chomwe a Nankhumwa adatenga choletsa chipani cha DPP kuwachotsa paudindowu.

Kuchotsedwa kwa chiletsoku kwadza pomwe a Nankhumwa sabata yatha alengeza kuti atula pansi udindo wawo ngati m’tsogoleri wa zipani zotsutsa boma m’nyumba ya malamulo pomwe ayambitsa chipani chawo cha People’s Development (PDP).

Kumayambiliro kwa chaka chino, Nankhumwa pamodzi ndi anthu ena khumi, anachotsedwa m’chipani cha DPP ati kamba kophwanya malamulo a chipanichi pomwe anali m’gulu la anthu omwe anayitanitsa komaso kupezeka pa nkumano wa waukulu popanda chilolezo cha m’tsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika. 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.