Bambo wafera pa tchalitchi cha Katolika pomwe amafuna kuba

Advertisement

Bambo wina wa zaka 27, wamwalira pomwe anagwidwa ndi nyesi ya magetsi pomwe amafuna kuba mtchalitchi cha Katolika m’boma la Mangochi.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Monkey Bay a Alice Sichali omwe azindikira malemuwa ngati a Geoffrey Matewere omwe akumana ndi zakudazi Lolemba pa 15 January, 2024.

A Sichali ati patsikuli, bambo Matewere anafika pa kachisi cha Katolika cha Nankhwali Parish chomwe chili kudera kwa mfumu yaikulu Nankumba m’bomalo ndicholinga chofuna kukaba zinthu zina.

Iwo ati mkuluyu atafika pa malo opatulikawo, anayamba kulimbana ndi “main switch” ya magetsi a pa kachisipa ndipo ali nkati mogwiragwira, anagwidwa nyesi ya magetsi ndipo anapezeka atafa.

Apolisi ati thupi la malemuwa omwe akuti anali odziwika bwino ndi nkhani za kuba mdelari, analipeza lili panja pa zenera la chipinda cha bambo mfumu, chomwe akuti ndichoyandikana ndi pomwe pali “main switch” yomwe amalimbana nayoyo.

Pakadali pano apolisi alangiza anthu kuti apewe mchitidwe oseweretsa, kugwira kapena kufuna kuba zopangizo za magetsi ndi cholinga chofuna kupewa imfa za ntundu ngati uwu.

Advertisement