Mnyamata wadzimangilira kamba kodzudzulidwa

Advertisement

Mnyamata wa zaka 18 zakubadwa yemwe anali mu fomu 1 wafa atadzinjatilira pa mtengo ku Mponela m’boma la Dowa kamba kakuti amadzudzulidwa pakhalidwe lake lochita  maubwezi ndi atsikana osiyanasiyana.

Nkhani yonse ikuti mnyamatayu yemwe dzina lake ndi Hastings Chakufuma, amakhala ndi azakhali ake ndipo anamudzudzula kamba ka khalidwe lopanga zibwenzi ndi atsikana osiyanasiyana.

Lolemba pa 8 January, Hastings anapezeka atafa ali lende mu mtengo. Malemuwa anasiya uthenga omwe analemba pakhoma lanyumba onena za zibwenzi zomwe anali nazo komanso zakudzudzulidwa kwake.

Ndipomneneri wa apolisi m’boma la Dowa a Macpastson Msadala ati achipatala anapeza kuti mnyamatayu atafa kamba kodzimangilira pa mtengo.

Hastings amachokera m’mudzi wa Mkunkhu, mfumu yaikulu Kaomba ku Kasungu.

Advertisement