Musawamvere, nkhanizo ndizopeka – SCOAN yayankha pa zomwe BBC yatulutsa za TB Joshua

Advertisement

…ati wofesa amayembekezera kukolora

…ati BBC ikuwawidwa ndi kukula kwa mpingo ngakhale TB Joshua anamwalira

Akuluakulu a mpingo wa Synagogue Church of All Nations (SCOAN) ku Nigeria, ati anthu asatekeseke ndi nkhani yomwe wayilesi ya BBC yatulutsa yokhudza malemu Mneneri TB Joshua ponena kuti nkhani zomwe wayilesiyi ikufalitsa, ndizopeka ndipo mpingowu sukuwadziwa anthu omwe amafusidwa mafuso ndi wayilesiyi.

Lolemba sabata ino, wayilesi ya BBC inatulutsa nkhani yomwe akuti ndizotsatira za kafukufuku yemwe inapanga kwa zaka ziwiri pa omwe malemu mneneri Temitope Balogun Joshua yemwe amadziwika kwambiri ndi dzina loti TB Joshua amkachitira zosayenera panthawi yomwe amatsogolera mpingo wawo wa SCOAN asanamwalire pa 5 June chaka cha 2021.

Malingana ndi zotsatira za kafukufuku wa BBC zomwe zagawida mumakanema atatu komaso zalembedwa ngati nkhani ndikuponyedwa pa intaneti, malemu mneneri TB Joshua ankazuza mamembala amumpingo mwawo komaso anthu ogwira ntchito awo, ankagona azimayi mowakakamiza kenaka ndikuwachotsetsa mimba, komaso akuti ankanamiza anthu pochita zozizwitsa zachinyengo, kungotchulapo zochepa chabe.

Koma malingana ndi chikalata chomwe mpingo wa SCOAN watulutsa Lachiwiri chomwe wasainira ndi ofalitsa nkhani za mpingowu a Dare Adejumo, nkhani zomwe wayilesi ya BBC yatulutsazi ndi bodza lankunkhuniza zomwe cholinga chake ndikungofuna kufowoketsa anthu komaso kunyazitsa ntchito zabwino zomwe malemu mneneri TB Joshua anachita asanatsogole ku ulemelero.

Kalatayi yati mpingowu ndiodabwa kuti wayilesiyi yomwe imatengedwa ngati namatetule pa ntchito zofalitsa nkhani, yaphwanya mfundo zofunika kwambiri pa ntchito yochita kafukufuku ndi kufalitsa kapena kuulutsa malipoti ponena kuti ntchito ya mtunduwu imafunika kumva mbali zonse komaso kulemekeza ma ufulu a mbali zonse zomwe mpingowu ukuona kuti sizinachitike mu nkhani yomwe yatulutsidwayi.

Mpingo wa SCOAN wati sumayenera kutaya nthawi yake ndikumayankha zomwe BBC yatulutsa koma yati yapanga izi ndicholinga chofuna kulimbikitsa anthu omwe atha kufooka ndikubwelera m’mbuyo pa moyo wa chikhilisitu kamba ka nkhani zopeka zomwe wayilesiyi yatulutsa, ndipo yanenetsa kuti BBC imayenera kupita ku mpingowu kuti ikafufuze yokha osati kudalira anthu omwe akuti mpingowu sukuwadziwa.

“SCOAN siyokonzeka kunyazitsa ulemu wake poyankha mtopola wa BBC. BBC sikanataya kalikonse ikanakhala kuti idapita kutchalitchi ngakhale kudzibisa ngati alendo kuti idziwe mwachindunji zomwe zikuchitika mu mpingo m’malo mongodziwa zomwe zikuchitika mu mpingo kudzera mwa anthu okhumudwawa omwe ena mwa iwo sadziwika nkomwe mu SCOAN monga tikuwonera m’magawo amakanema omwe atulutsidwawo. Ena mwa iwo ndiwodziwika kwambiri ndi nkhani za anthu omwe amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Zonse zomwe BBC yasonkhanitsa pamodzi ndizachilendo ku mpingo wa SCOAN.

“Chinthu chinanso chosamveka bwino pa nkhaniyi ndi mawu omwe BBC ikuti munthu wa Mulungu-yu anakhudzidwa ndi nkhanza zonsezi kwa zaka zoposa makumi awiri (20). Kodi zimenezi zingatheke bwanji m’dziko loyendetsedwa ndi malamulo ngati Nigeria? Komanso anthu opelekera umboniwa anali kuti nthawi yonseyi? Amadikira kuti TB Joshua amwalire kaye kenaka ndikudzidzimuka? Opusa yekha ndi amene angakhulupilire izi. Izi sizichititsa manyazi kokha komaso ndi ndizovetsa chisoni kuti zikuchokera kwa olemba nkhani omwe amatengedwa ophunzitsidwa bwino,” atelo a Adejumo mukalatayo.

Mpingowu wati ukuganiza kuti ogwira ntchito ku wayilesiyi apanga izi kamba kowawidwa ndikukula kwa mpingo wa SCOAN zomwe akuti nkutheka samayembekezera potsatira imfa ya malemu mneneri TB Joshua koma mpingowu wanenetsa kuti chilichonse chochokera kwa Mulungu sichikhoza kuzulidwa ndi munthu aliyense.

Kalatayi yatsindikaso kuti kuzunzidwa kwa nthumwi zaumulungu kapena atumiki a Mulungu sikuli kwachilendo m’mbiri ya anthu ponena kuti kaleloso anthu ena ananyengereredwa ndi kunenera umboni wabodza, owopsa ndi owononga, ndipo mpingowu wachenjeza wayilesi ya BBC ponena kuti aliyese wofesa mbewu iliyose amayembekezera kukolora.

“CHINTHU chimodzi ndi chofunikira kwambiri komanso chomwe aliyense wopanga nkhani ayenera kudziwa: palibe amene angathe kuthawa kukolola zinthu kuchokera ku mbeu iliyonse yomwe wabzala m’chilengedwe. Kunena zoona, zili mu chifuniro cha Mulungu kuti wobzala woteroyo kudzera m’mawu ake, zochita, zolembedwa kapena zochita sizidzakhala zaufulu kufikira anthu omwe adawasokeretsa atakhala mfulu.

“Ichi ndichifukwa chake tisalole kutengeka ndi nyengo ililonse pofuna kusamala phindu lapompopompo chifukwa zotsatira zake zitha kukhala imfa. Atolankhani aku BBC omwe akuti afufuza zomwe ankapanga TB Joshua, ayenera kuweramitsa mitu yawo mwamanyazi monga atolankhani mu ulendo wawo wopeka zopanda pake,” yateloso mbali ina ya kalata ya SCOAN.

Kupatula apo, mpingowu wati ndiwodabwa kuti wayilesi ya BBC siyinatchule nkazi wa malemu TB Joshua, a Evelyn pa zonyasa zomwe wayilesiyi ikuti amunawo ankapanga,  ponena kuti palibe mkazi yemwe angakhale chete pomwe mamuna wake akumapanga zodama ndi akazi ena, ndipo mpingowu wati ichi ndichitsimikizo choti nkhanizi ndizopekadi.

Advertisement