Agalu achizungu alikhwira ndi kupha mwana

Advertisement
A 7-year-old girl identified as Miracle Evence has died after two German Shepherds left their owners house and attacked her.

Pena munthu ukaganiza kwambiri ukumati mwina bolaso kuweta agalu athu omwewa achikudawa. Komabe kuganiza izi ndi kamba kamkwiyo nde tiyeni tizisiye naye zimenezo, koma funso nkumati alira bwanji makolo ake a Miracle omwe amawona tsogolo lokoma mwa mwana wawo Miracle.

Nanga anzake adziti chiyani kwenikweni pomwe atangomaliza kusewera phada komaso fish-fish limodzi, dzuwa lisanalowe awuzidwa kuti nzawoyo watsogola ku ulemelero. Kodi nanga anawa akaona galu aliyese adzimva bwanji?

Awa ndi ena mwa mafuso amene munthu atha kumadzifusa akalingalira kwambiri za ngozi yowopsa yomwe yagwa m’mudzi mwa a Chikuluti dera la mfumu yaikulu Mponela m’boma la dowa

Lachitatu sabata ino pa 3 January, 2023, linacha monga mwa masiku onse m’mudzi mwa Chikuluti ku Mponela ndipo monga mwa nthawi zonse, bambo ndi mayi Evance anali kuthamanga-thamanga podziwa kuti sikadza kokha kamawopa kulawura.

Mbali inayiso mwana wawo wa nkazi wa zaka zisanu ndi ziwiri (7), Miracle amachita zonse monga mwa nthawi zonse; kusewera ndi anzake, kutumikira ntchito za pakhomo osadziwa chakudza kutsogolocho, paja akuluakulu anali mphuno salota.

Momwe madzulo a tsikuli, nkhope zosangalala zija zinali zitasintha kudelari, thambo lakuda linawakuta, misozi yosakata m’masaya mwawo inatsika; mwana yemwe ena anamuona akusewerayo, mukuphethera kwa diso anali atayamba kutchedwa malemu.

Koma zakhala bwanji kwenikweni, mwanayu ndamuona pompano akusewera? Anthu anayamba kufusana. “Agalu akumpanda ukoko akuti amuluma,” m’modzi anayankha kwina ku akusisima kamba kachisoni, mbali inayi misonzi ikulakatika, kutsetselekera m’masaya.

Koma kwenikweni zakhala bwanji? Malinga ndi mneneri wa polisi ya Mponela a MacPatson Msadala, eniwake a nyumba ina yomwe ili ku mpanda, anali akuchokera ku ntchito madzulo a tsikuli ndipo pamene anatsekulilidwa chipata kuti alowe ndi galimoto yawo kumpandako, agalu awo awiri achizungu (German Shepherd) anatuluka kumpandako.

Funso nkumati kodi mesa agalu owopsa ngati awa amayenera kumangidwa pa tcheni kuopa malodza ngati awa? Kaya, nafe sitikudziwa kuti eni zilombozi anazisiyilanji zosamangidwa pa nthawi yomwe dzuwa linali lisanalowe. Kapena anapanga dala? Mmh ayi, tisaganize kwambiri.

Chipata cha mpandawu chitangotsekulidwa, pomwepo zilombo ziwiri mwa zinayi zomwe zinali ku mpandaku zinaliyatsa liwiri la mtondo wadooka kutuluka panja ngati kuti zawona mbava.

Izo zinathamangila kunja komwe zinapeza Miracle akungodzisewelera ndipo zinamulikhwira mwana osalakwayo ndikumuluma zodetsa. Miracle analira movetsa chipani. “amayi, amayi, amayi,” koma panalibe thandizo la nsanga kufikira agaluwa anamuvulaza kwambiri.

Momwe anthu amathamangira ku malowa atamva mfumu yamwanayu, agaluwa anali atamuvulaza kale modetsa nkhawa ndipo pomwe anatengedwela ku chipatala cha Mponela, madotolo anatsimikiza kuti mtsikanayu watisiya kamba kotaya magazi ochuluka zomwe ndi chifukwa cholumidwa ndi a galu olusawa.

Posakhalitsa, anthu olusa omwe anakhamukira ku malo angoziwa kudzadzionera okha malodzawa, anatenga miyala ndi zigwandali ndikuyamba kupha zilombozi ndipo poti akulu a kale anati kalulu akanyata pa chitsamba umamenya ndichitsamba chomwecho, a galu enaso awiri omwe sanapange nawo chipongwechi koma anali  nawo kumpandako, anaphedwera limodzi, kupangitsa chiwerengero cha a galu ophedwa kuti chifike pa anayi.

Mbali inayi, eni ake zifuyozi akwidzingidwa zingwe kamba kosasamala zilombozi zomwe zapangitsa kutaya moyo wa mwana osalakwa, Miracle.

Masana a Lachinayi pa 4 January, 2024 anali osayiwalika m’mudzi mwa Chikuluti kamba koti anthu atsanzikana ndi Miracle yemwe wayenda m’manja pomwe anali ndi mphamvu zonse. Dziko laluza nzika yofunika yomwe ikanatha kudzalitukura munjira inayake.

Advertisement