Pitani ndakukhululukirani koma musakachimwenso: Chakwera wakhululukira akaidi


Pitani ndakukhululukirani koma musakachimwenso: Chakwera wakhululukira akaidi- Malawi24

Akayidi okwana 48 tsopano akhala akusimba lokoma kutsatira mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera  wakhululukira ndikumasula akayidiwa mnyengo ino  yachikondwerero cha khilisimasi komanso chaka chatsopano.

Malingana ndi chikalata chomwe atulutsa a Oliver Kumbambe yemwe ndi mlembi wamkulu muunduna wazachitetezo, mtsogoleri wa dziko lino wakhululukira akayidiwa omwe tsopano agwira theka lazaka zomwe khothi lidawagamula.

Mwa akayidi ena omwe  a Chakwera awakhululukira ndi achikulire ndi akayidi achizimayi omwe adatsekeredwa  mu ndende pamodzi ndi makanda.

Chaka chomwe chino m’mwezi wa April,  mtsogoleriyu adakhululikiranso  akayidi 200 mu nyengo ya pasaka ya chaka chino ndipo m’modzi mwa okhululukidwa adali John Mussa nyamata yemwe adapezeka ndi chamba.

Wolemba: Ben Bongololo

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading