Sukulu ya University of Livingstonia yakweza fizi


University of Livingstonia

Sukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia (Ekwenden Campus) yalengeza kuti yakweza sukulu fizi ndipo izi zikhudza ophunzira amene akudzayamba kumene komanso omwe omwe akupitiliza maphunzilo awo pasukuluyi.

Malingana ndi chikalata chomwe sukuluyi yatulutsa, kusinthaku kuyamba mu January 2024, mwezi omwe uyambike sabata la mawa lolemba.

Ndipo kubweraku kuli motere: Ophunzira omwe ndi okhalira pasukulu pomwepo azilipira K794,100, oyendera (Off Campus) 694,100 pamene a ODL adzilipira K211,200 pa semisita.

Sukuluyi yati yakweza ndi 10 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse yomwe ophunzirawa amayenera kulipira ngati sukulu fizi.