Chipatala cha Balaka chayamikira Ngalande popeleka galimoto

Advertisement
Ambulance

Pali chiyembekezo chachikulu kuti ntchito za umoyo m’boma la Balaka zipita patsogolo kutsatira thandizo la galimoto za ambulansi ziwiri zomwe phungu wa dera la kumpoto m’boma la Balaka, Tony Ngalande, wapeleka pa chipatala chachikulu cha bomali.

Malingana ndi mneneri wa chipatalachi, Mercy Nyirenda, thandizoli lafika mu nthawi yomwe ngozi zosiyanasiyana zimachulukira.

“Monga mukudziwa, tili mu nyengo ya zisangalalo ndipo mu nyengo imeneyi, ngozi zosiyanasiyana zimachuluka. Izi zimapangitsa kuti tizilandira anthu ovulala ambiri kuno ku chipatala  cha Balaka,” adafotokoza Nyirenda.

Iwo adayamikira phunguyi ponena kuti thandizoli sikuti lifikira anthu okha okhala mu dera la kumpoto kwa bomali, koma lifikiranso anthu ambiri m’bomali omwe amazapeza thandizo la mankhwala pa chipatalachi.

M’mawu ake, phunguyi adati ndi odzipeleka pothandiza kutukula ntchito zosiyanasiyana za chitukuko kuphatikizapo ntchito za umoyo.

A Ngalande ati agwiritsa ntchito ndalama pafupifupi K60 miliyoni pogula ma ambulansiwa.

Advertisement