Madotolo konzekani: Boma lilemba anthu ogwira ntchito m’zipatala oposera 5, 000

Advertisement
Mzimba District Hospital

Pamene boma likukonzekera kulemba anthu ogwira ntchito mzipatala zaboma oposera 5,000, mkulu yemwe amayankhulapo pa nkhani za umoyo wayamikira boma la a Lazarus Chakwera kamba kochita chothekera poonetsa kuti anthuwa alembedwe ntchito.

Vuto lakuchepa kwa anthu ogwira mzipatala mdziko lino ndi mwa limodzi lomwe likulowetsa pansi ntchito za umoyo mdziko muno kotero a George Jobe ati izi zithandiza kuchepetsa ena mwamavuto omwe mzipatala za dziko lino zikukumana nawo.

Iwo anapitilizanso kupempha boma kuti likuyenera kuwaganizira ogwira ntchitowa pochita chothekera kuti akuyenera kukweza malipiro awogwira ntchito.

Kuwonjezera apo iwo anatinso nkofunikira kuti boma lichiteponso kanthu powonetsetsa kuti mankhwala mzipatala za dziko lino akupezeka powonjezera ndalama zogulira mankhwalawa.

Malingana ndi unduna wa za umoyo mdziko lino, ntchito yolemba ogwira ntchito m’zipatala mdziko muno ichitika ndi thandizo lochokera ku global fund.

Advertisement