Ma bishopu a mpingo wa Katolika pansi pa bungwe la Episcopal Conference of Malawi (ECM), ati zomwe alamula kuti a nsembe asamapeleke mdalitso uli onse kwa anthu okwatilana amuna kapena akazi okhaokha, sizikutanthauza kuti iwo awukira mtsogoleri wa mpingowu Papa Francis.
Sizikutanthauza kuti mpingowu waloleza maukwati a amuna kapena akazi okhaokha ndipo anenetsa kuti palibe wa nsembe amene aloledwe kudalitsa maukwati oterewa kuno ku Malawi.
Nkhaniyi inayamba Lolemba pa 18 December kutsatira kalata yomwe mtsogoleri wa mpingowu a Papa Francisco anatulutsa yomwe mwana zina imapeleka chilolezo kwa ansembe kuti atha kumapeleka mdalitso pa anthu okwatilana amuna kapena akazi okhaokha.
Potsatira momwe anthu anayankhulira zokhudza kalatayi, bungwe la ECM kudzera mu chikalata chomwe linatulutsa Lachiwiri, lati zikuoneka kuti panali kusamvetsetsa pa nkhaniyi ndipo pofuna kusabweletsa chipwilikiti mumpingo, alamula kuti wa nsembe aliyese wa mpingowu mdziko muno asapeleke mdalitso uli onse kwa anthu okwatilana amuna kapena akazi okhaokha.
Izi zapangitsa kuti anthu ochuluka ayambe kuganiza kuti mpingo wa Katolika kuno ku Malawi kudzera kwa mabishopuwa pansi pa bungwe la ECM, wawukira mtsogoleri wa mpingowu pa dziko lonse, Papa Francisco.
Koma poyankhula ndi wayilesi ya Zodiak mu pologalamu yapadera yomwe yaulutsidwa Lachitatu pa 20 December, 2023, bungwe la ECM lati zomwe lalamula sizikutanthauza kuti iwo awukira koma ati akufuna kuti pasakhale chipwilikiti mu mpingowu kamba ka nkhaniyi.
Mlembi wa ECM bambo Vereliano Mtseka anatsindika kuti akuona kuti zomwe anena Papa zitha zibweretsa chisokonezo ku chikhalidwe cha mdziko muno chifukwa choti maukwati a anthu ofanana ziwalo amatengedwa achikunja komanso osaloredwa.
“Kalata iyiyi (ya Papa Francisco) siyikulamula koma ikudziwitsa nde zomwe tanena kuti wa nsembe aliyese asapeleke mdalitso uli onse kwa anthu ofanana ziwalo amene ali pa ubwezi kamba koti tayang’anira chikhalidwe chathu kunoku. Ndinafotokoza kuti mayiko ena anthu amatha kudalitsitsa galu, koma ine sinadalitseko galu chifukwa anthu kuti andione ndikudalitsa galu, sangandivetse.
“Nde tikunena kuti pofuna kusabweretsa chisokonezo pakati pa akhilisitu athu, taona kuti ndi bwino kuti zimenezizi tisapange, tingopitiliza m’mene takhala tikupangira m’mbuyomu. Palibe kuukira kwina kulikose koma kuti tikufuna kungowthandiza anthu kuti asasokonekere popeza kuti anasokonekera kale kalatayi itatuluka. Pakadali pano ma bishopu anena kuti zimenezizi ife sitipanga,” watelo Mtseka.
Iwo anapitilira ndi kufotokoza kuti kalata ya Papa Francisco , mabishopu anzawo mmaiko ngati Zambia, Ethiopia ndi ena ambiri, ayankhulaposo molingana ndi zikhalidwe za m’maiko mwawomo ndipo anenetsa kuti salola kuti mpingowu uzichita zoipa kamba kofuna thandizo.
“Ukwati wa amuna Karena akazi okhaokha mumpingo wa Katolika sumaloledwa, ndipo chiphuzitso chathu chimavomera ukwati wake pakati pa mayi ndi bambo. Ifeyo taima nganganga pazimene mpingo umaphuzitsa zokhudza ukwati ndipo palibe chimene tingasinthe china chili chose chifukwa zimene timaphuzitsa ndi mawu a Mulungu. Ndikwabwino kukhala osauka kusiyana 0 zofuna zawo, ifeyo sitidzalora kugulitsa chikhulupilira chathu chifukwa cha chuma,” wateroso Mtseka.
Iwo ati alimba mtima kulamula nsembe kuti asapereke mdalitso uli onse kwa anthu okwatirana amuna kapena akazi okhaokha, ponena kuti kalata ya Papa Francisco inawapatsa ufulu opanga kapena kusapanga zomwe anenena zokhudza mdalitso.