Tavomera ndipo zatha basi – yagonja Wanderers


Malawi Football players

Timu ya mpira wa miyendo ya Mighty Mukuru Wanderers, yati yavomeleza chilango chomwe yapatsidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi (FAM) ndipo yati siyipangaso apilu.

Izi zikudza pomwe komiti yomva ma apilu (appeal) ku bungwe la FAM Lachinayi yatulutsa chigamulo pa nkhani yomwe timu ya Wanderers inakadandaula italephera kukhutitsidwa ndi chigamulo cha komiti yoyendetsa mipikisano ku bungweli pa nkhani ya masewero omwe anathera pa njira ndi timu ya Silver Strikers mwezi wa September mu chikho cha Airtel Top 8.

Mwazina, komiti ya ma apilu ku FAM, yagamula kuti timu ya Noma inaluza masewero amene anathera panjira ndi zigoli ziwiri kwa duu komaso inaluza 2:0 masewero ake achiwiri ndi Silver omwe timuyi inakana kukasewera pa bwalo la Kamuzu munzinda wa Blantyre, zomwe zikutanthauza kuti Wanderers yaluza 4:0 pa masewera onsewa.

Kupatula apo, komiti ya ma apilu ku FAM yachepetsa chindapusa cha 24 miliyoni kwacha chomwe timu ya Wanderers inalamulidwa kulipira ndi komiti yoyendetsa mipikisano ku bungweli ndipo tsopano timuyi ikuyenera kupeleka ndalama zokwana 22 miliyoni kwacha ngati chindapusa ndipo ina mwa ndalamayi ikagwira ntchito yokozetsera mipando yomwe inawonongeka pa bwalo la Bingu munzinda wa Lilongwe.

Poyankhapo za chigamulo chatsopanochi, timu yovala makaka a “blue”yi kudzera mukalata yomwe yatulutsa Lachinayi, yomwe wasainira ndi mlembi watimuyi a Chancy Gondwe, yati yachilandira bwino chigamulochi ndipo ilibeso malingaliro ofuna kukasumaso.

“Talandira chigamulo chochokera ku komiti ya apili ku bungwe la FAM. Mukudziwitsidwa kuti ngati Wanderers tavomera chigamulo chomwe ndichochokera ku bwalo lamilandu lomaliza. Ngakhale timafuna kutengera nkhaniyi ku Court of Arbitration for Sports (CAS), tikuwona kuti tiyenera kuvomereza chigamulochi mokomera mpira m’dziko muno,” yatelo Wanderers mukalatayo.

Timuyi kudzera mu kalatayi yati nthawi yakwana tsopano yoti njira yothetsera mikangano pansi pa malamulo a bungwe la FAM iwunikiridwenso ndicholinga choti mavuto omwe avumbulitsidwa pa nthawi ya mlandu wawowu, athetsedwe kuti masewero a mpira wa miyendo apite chitsogolo.

Masewero oyamba a Silver ndi Wanderers mu chikho cha Airtel Top 8, anathera panjira pamene oyimbira Godfrey Nkhakananga anavomeleza kuti ‘Ma Bankers’ achinya chigoli chachiwiri pa nthawi yomweso iyeyo anali ataimba kale kuti panali kukokana kokana.