Anjatidwa kamba kosayendetsa bwino ndalama

Advertisement

Apolisi m’dziko lino anjata a Shirieesh Betgiri yemwe ndi mkulu wapampando wakale wa kampani ya Salima Sugar kamba kokhudzidwa pa mlandu wakatangale wa ndalama zoposa K50 billion

A Peter Kalaya omwe ndi mneneri wa apolisi m’dziko muno atsimikiza zankhaniyi ndipo iwo ati izi zadza pamene boma idachita kafukufuku ndipo malipoti adaonetsa kuti anthu ena adabera boma kudzera ku kampani ya Salima Sugar.

Iwo anapitilizanso kunena kuti iwo atenganso zilolezo zina zinayi zowonjezera kuti anjate omwe akukhudzidwa pazachinyengozi.

M’masiku apitawo, kudali Mkakamizo ofuna kuti Boma la Malawi lichotse wapampando wa kampaniyi, a Wester Kosamu kamba kowululidwa za kusayendetsa bwino ka ndalama pakampaniyo.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement