TNM yakweza mitengo ya mabandulo ake oimbira komanso a intaneti

Advertisement
TNM Data prices

Patangopita masiku ochepa kampani ya lamya za m’manja ya Airtel Malawi itakweza mitengo yogulira ma bandulo ake, nayonso TNM yakweza mitengo yake ndi K20 pa K100 iliyonse.

Malingana ndi uthenga omwe kampaniyi yatulutsa yati yachita izi kutsatira kugwa kwa mphamvu ya ndalama ya kwacha.

Mwachitsanzo Pamtsetse bundle wa masiku 7 yemwe amagulidwa pa mtengo wa K1199 ndipo amapereka 2.2gb azigulidwa pamtengo wa K1679, whatsapp bundle ya K770 ya mwezi yopereka 650mb pano izigulidwa pa K999 ndipo izipereka 600mb.

Tnm yachotsanso mabandulo ena oimbira komanso a internet Mtolo 600 wa K600 wa sabata omwe umapereka mphindi 45, Smart Whatsapp Weekly wa K499 yemwe amapereka 300mb kugotchulapo ochepa.

Ndipo kusintha kwa mitengoku kuyamba kugwira ntchito mawa pa 15 December 2023.

Masiku apitawo kampani ya Airtel inakweza mitengo ya ma bandulo ake oimbira ndi K15 pa K100 iliyonse komanso a internet ndi K20 pa K100 iliyonse ati chifukwa chakukwera kwa mafuta agalimoto komanso mtengo ogulira magetsi kutsatira kugwa kwa kwacha.

Advertisement