Chakudya komanso magetsi zavuta pa sukulu ya Mulunguzi

Advertisement

Kusowa kwa chakudya komanso kuthima kwa magetsi kwasokoneza maphunziro pa sukulu ya sekondale ya Mulunguzi mu boma la Zomba.

M’phunzitsi wankulu wapasukuluyi a Silk Kadwala atsimikidza zankhaniyi ndipo ati pakali pano ana akuwalembetsa mayeso pofuna kuti pofika Lachisanu sabata ino ophunzirawa akhale atachoka pasukuluyi chifukwa zinthu zafika poyipa kwambiri.

A Kadwala ati magetsi adathima Lamulungu ndipo patha masiku anayi magetsi asakuyaka chifukwa chosowa ndalama yokalipira ku Escom.

Iwo ati idzi zikuchitika chifukwa Boma likulephera kupereka ndalama zogwilitsira ntchito zina pasukuluyi (ORT) ndipo ndalama zomwe akhala akugwiritsira ntchito ndi zomwe ophunzira amalipira ndipo ati pakali pano ndalamazi zatha.

“Ndalama zomwe timalandira kuchokera ku Boma zimathandidza kugulira zina ndi zina monga kulipira magetsi komanso madzi choncho tikumatenga ndalama zomwe ana ognera pa sukulu amalipira ndi kugwiritsa ntchito koma sidzikukwanira,” adatero a SiKadwala.

Ophunzira omwe sadafune kuti tiwatchule dzina ati moyo wafika povuta pasukuluyi mokuti ophunzira ena omwe sadatsilidze kulipira sukulu fees akugona ndi njala.

Iwo adandaulanso kuti akumalemba ma sabujekiti atatu kapena anai patsiku pofuna kuti atsilidze mwachangu kulemba mayeso.

Tidafuna kumva zambiri kuchokera kwa mmeneri wa Unduna wa zamaphunziro Mphatso Nkuonera koma watiuza kuti timupatse nthawi kuti ayambe wafufuza kaye.

Advertisement