Ulendo wa ku Israel wasintha

Advertisement
Israel Malawians

Ulendo wa achinyamata omwe amayenera kunyamuka lero lachitatu kupita mdziko la Israel wasinthidwa.

Achinyamata okwana 200 omwe amayenera kukwera ndege lero pa bwalo la ndege la Kamuzu International ku Lilongwe ulendo okagwira ntchito ku Minda ya mdziko la Israel wasinthidwa.

Malinga ndi uthenga omwe Malawi24 yapeza kuchokera ku bugwe lomwe likuyendetsa za izi la Lions Human Resouces Management Services, ulendowu wasunthidwa kufika mawa Lachinayi pa 14th December 2023.

Gululi lomwe ndi lachiwiri lidzanyamuka lachinayili nthawi ya 1 koloko masana kupita kukagwira ntchito, ndipo akulu akuluwa omwe akuyendetsa za achinyamata olembedwa ntchitowa ati gulu lachiwiri likapita pabweranso gulu lina la chitatu.

Mneneli wa mu unduna wa Zantchito a Nellie Kapatuka anatsimikira nyumba ina yolemba nkhani kuti ulendo wachiwili wa achinyamatawu ulipodi

A kapatuka anati Ndegeyi imayenera kunyamuka lero lachitatu 7 koloko m’mawa.

Advertisement