Achinyamata ena 200 wapsa wa ku Israel mawa

Advertisement
a plane from Israel arrived in Lilongwe where it picked up over 200 young Malawians who have since arrived in Israel today.

Boma latsimikiza kuti gulu la chiwiri la achinyamata okwana 200 linyamuka m’dziko muno lachitatu kupita kukagobola ntchito zakumunda m’dziko la Israel.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani ku unduna wazantchito a Nellie Kapatuka omwe awuza nyumba zina zofalitsa nkhani m’dziko muno kuti ndege yomwe ikuyembekezeka kunyamula anthuwa, ifika m’dziko muno lero lachiwiri masana ano

Malingana ndi a Kupatuka, achinyamata omwe akunyamuka nawo kupita ku Israel mugawo ili lomwe ndi lachiwiri, alipo okwana 200 ndipo a ndege yomwe anthuwa akwere, ikuyembekezeka kunyamuka 7 koloko m’mawa wa lachitatu pa 13 December, 2023 kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu munzinda wa Lilongwe.

Gulu loyamba la achinyamata omwe akukagwira ntchito zakumundazi m’dziko la Israel linanyamuka m’dzikomuno pa 25 November chaka chino ndipo tikuyankhula pano anthuwa ali m’dzikolo kugwira ntchito zakumunda zosiyanasiyana.

Poyamba nkhani ya ulendo wa achinyamatawa, 8nadzetsa mapokoso kamba koti mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma mu nyumba ya Malamulo, a Kondwani Nankhumwa, anapempha boma kuti lifotokoze bwino ngati anthuwa akupitadi m’dzikolo kukagwira ntchito zakumunda osati nkhondo yomwe ilipo mbali ina ya dzikolo.

Koma mitima ya anthu ambiri inatsika pansi pomwe boma linabwera poyera ndikutsindika kuti achinyamatawa sakupita ku israel kuthandizira pa nkhondo yomwe ilipo ndi dziko la Palestine koma kuti akukagwira ntchito zakumunda.

Advertisement