Bon Kalindo wamangidwanso bwalo ku Zomba litamupatsa belo

Advertisement
Bon Kalindo has been arrested several times since he started conducting anti-government demonstrations


Bwalo la Principal Resident Magistrate ku Zomba lapereka belo kwa mkulu wa Bungwe la Malawi First a Bon Kalindo koma apolisi amanganso a Kalindo atangotuluka mu bwalo la milandu pankhani yokhudza zipolowe za ku Mangochi pa nthawi yomwe adachititsa mademo.

Bwaloli linakana pempho lomwe adapempha woyimira Boma pamilandu loti a Kalindo asawapatse belo kuwopa kuti angakasokoneze umboni ndipo bwaloli lati woyimira Boma pamilandu sadafotokoze momveka bwino kuti akasokoneza bwanji umboniwo.

Bwaloli lati munthu aliyense ali ndi ufulu wopatsidwa belo potengera momwe malamulo oyendetsera m’dziko lino akunenera.

Woweluza mulanduwu Principal Resident Magistrate Martin Chipofya wapereka belo kwa Bon Kalindo ndipo lawalamula kuti apereke chikole cha 400,000 kwacha komanso azikawonekera kulikulu la apolisi mchigawo chaku m’mawa kamodzi pakatha masiku 14.

Koma a Kalindo atangotuluka mu bwalo lamilandu apolisi awamanganso powaganizira kuti adayambitsa zipolowe ku Mangochi panthawi yomwe adachititsa mademo.

Pakali pano apolisi awatenga a Kalindo kupita nawo ku boma la Mangochi.

Advertisement