Muimitse masewero apo bii ife sitikapezeka – yanenetsa Wanderers

Advertisement
Mighty Wanderers

Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yanenetsa kuti ngati bungwe la Football Association of Malawi (FAM) siliyimitsa masewero ake ndi timu ya Silver Strikers lero, iyo siyikapezeka pa masewerowa kufikira chilungamo chidziwike.

Dzulo lachiwiri, timu ya Wanderers inapempha bungwe la FAM kuti liyambe layimitsa kaye masewero ake achibwereza ndi timu ya Silver mu mpikisano wa Airtel Top 8 kamba koti yati ikufuna kuti chilango chomwe yapatsidwa ndi bungweli chiunikilidwenso.

Koma poyankhapo pa pempho la Wanderers, bungwe la FAM kudzera mu kalata yomwe linatulutsa lachiwiri lomwelo yomwe inasayinidwa ndi a Alfred Gunda, linakana pempholo ndipo linalamula kuti masewero achiwiri a timu ya Wanderers ndi Silver, akhalapobe lachitatu lino pa bwalo la masewelo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre monga momwe anakozedwera poyamba.

Nayo Wanderers kudzera mwa m’modzi mwa akuluakulu ake a Roosevelt Mpinganjira, inatulutsa kalata ina yoyankha pakukanilidwa pempho ndi bungwe la FAM ndipo timuyi yati ndiyodabwa ndi yankho lomwe bungwe loyendetsa mpirali lawayankha.

Timuyi yati ikuona kuti ndikofunika kuti masewero ake ndi Silver ayimitsidwe kaye podikira kumva ndi kugamula apilo yawo yomwe akufuna kupanga pa chilango chomwe timuyi inapatsidwa potsatira chipwilikiti chomwe chinachitika pa bwalo la masewero la Bingu ku Lilongwe mwezi wa September chaka chino.

“Wanderers FC ikupempha komiti ya FAM ya mpikisano kuti ipewe kukhumudwitsa dala timu yathu popanga zinthu zosayenera komanso zopanda nzeru pomwe tikutsata malamulo omwe alipo komanso ufulu wathu wochita apilo mumpikisano wa mpira. Tikudziwa kuti nkhaniyi ili kunja kwa komiti yoyang’anira mpikisano chifukwa tsopano ikuyendetsedwa ndi mabungwe a FAM.

“Pofuna kuwonetsa chilungamo pankhaniyi, Mighty Mukuru Wanderers FC tikupempha bungwe la FAM kuti liyimitse kaye masewero athu achiwiri pokhapokha ngati apilo yomwe tikudikila kuti tipange itakanidwa ndi komiti ya ma apilo, apo bii timu yathu sikasewera masewerowa,” yatelo Wanderers.

Masewero oyamba ampikisano wa Airtel Top8 a pakati pa Wanderers ndi Silver anathera panjira pomwe kunabuka mapokoso potsatira chiganizo cha oyimbira Godfrey Nkhakananga yemwe anavomereza kuti Silver yachinya chigoli chachiwiri pomwe iye yemwe anali ataimba kale kuti panali kukonakokana.

Advertisement