Ophunzira ku UNIMA akusowa ndalama ya chakudya komanso yolipilira nyumba


Unima Malawi

Ambiri mwa ophunzira omwe ali pangongole yaboma pasukulu ya ukachenjede ya UNIMA ati alipachiopsezo chosiyira maphunziro awo panjira kaamba kosowa ndalama yogulira zakudya komanso kulipilira nyumba zomwe iwo amakhala ngakhale kuti anasayinira ndalamayi ndibungwe lopereka ngongole la Higher Education Students’ Loans Board.

M’modzi mwa ophunzirawa yemwe ali mchaka chachinayi chamaphunziro ake pa sukuluyi koma sanafune kutchulidwa dzina wati pakadali pano ophunzirawa athamangitsidwa mu nyumba zomwe amakhala kaamba kolephera kulipira.

“Tikuvutika kwambiri. Tathamangitsidwa m’manyumba omwe timakhala chifukwa tikulephera kulipira. Tikusowa chakudya ndipo maphunziro athu sakuyenda chifukwa tilindimaganizo oti kodi ndalama tiyipeza bwanji. Ambiri mwa ife akuchokera m’mabanja osauka omwe sangakwanitse kutigulira zakudya ndi zina zotero, “anatero ophunzirayi.

Poyankhapo ngati iwo anakumana ndi wina aliyense kuti awathandize zavutoli, ophunzirayi anati :”Tinasainilana ndi bungwe loona za ngongole la Higher Education students’ Loans and Grant Board ndipo zikalata anapititsa kuma ofesi awo koma chodabwitsa ndichakuti akumatiuza kuti ena mwa ife zikuonetsa kuti sitidasainile.Tayankhulanakoso ndi mtsogoleri wa ophunzira pasukulu pano komanso ma email takhala tikutumiza kwa dean of students kuti atithandize monga mmene tinauzidwila ndi anthu ogwila ntchito ku loans board kuti tidzele kumeneko pofuna kuti atithandize koma mpaka pano sitikuona kochokela yankho.”

Choncho ophunzirawa aopseza kuti ngati akuluakulu asukuluyi sachitapo kanthu pankhaniyi iwo azikagona kuma ofesi awo ogwira ntchito.

Olemba: Chisomo Phiri