Boma lapereka chimanga ndi ndalama kwa omwe adakhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy

Advertisement
Maize donation to Cyclone Freddy survivors

Kutsatira mavuto omwe alipo kamba ka namondwe wa Freddy yemwe adaononga mbewu ndikuyika a Malawi ochuluka munjala yadzaoneni, tsopano boma layamba kugawa chimanga komanso ndalama m’madera omwe adakhudzidwa.

Ntchito yopereka thandizoli yayambira mu mzinda wa Zomba komwe ntchitoyi yakhazikitsidwa. A Konja Mikana, m’modzi mwa omwe alandira nawo thandizoli, ati tsopano vuto lanjala lichepa.

Archangel Bakolo yemwe ndi mkulu woyendetsa ntchito za Khonsolo la mzindawu wayamikira komanso kuthokoza boma kamba kokwanilitsa pangano lake.

Yemwe ndi wachiwiri kwa mfumu ya mzindawu, a Munira Bakali, achenjeza anthu omwe ali ndi khalidwe logulitsa katundu akalandira thandizo ndipo ati aliyense amene angapezeke akugulitsa chimangachi achotsedwa pa mdandanda wathandizoli ngati njira imodzi yowonetsetsa kuti amene akulandirawa ndiwoyenerela.

Maanja ankhaninkhani akuyembekezereka kuthandizika mu ndondomekoyi mumzindawu  maka mumwezi uno mpaka kufika chaka cha mawa mumwezi wa Marichi mbewu zakumunda zitakhwima.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement