Mayi wazaka 38 yemwe dzina lake ndi Takondwa Banda ali m’manja mwa a polisi ku Kasungu kogwirira mwana wammuna wazaka 16 ndi kumupatsila matenda opatsilana pogonana.
Mneneri wa polisi ya Kasungu Joseph Kachikho wati izi zinachitika mu mwezi wa Okotabala chaka chino.
A Kachikho ati mnyamatayu analembedwa ntchito yogwira kumunda kwa a Banda ndipo amagona ku khitchini.
Kenaka tsiku lina, Banda anauza mnyamatayu kuti akagone m’nyumba mwake. Apa Banda anayamba kumuonetsa mwana uja makanema olaula kenaka anamukakamiza kugona naye.
A Banda anapanganso zomwezi tsiku lina ku tchire ndipo mwana uja anakatula nkhaniyi ku polisi.
Malingana ndi a Kachikho, mwanayu atamutengera ku chipatala cha Kasungu anamupeza ndi nthenda ya chindoko yomwenso mayi Banda anawapeza nayo.
Mayi Banda akuyembekezeka kuonekera ku bwalo la milandu pa mulandu wogonanana ndi mwana.