Zipolowe za ku Limbe ndinanenera kalekale – watelo mneneri Mtupa

Advertisement
Malawi Vendors attacking a city council vehicle in Blantyre

Mtsogoleri wa mpingo wa Holy Palace Cathedral International, mneneri Rodrick Mtupa, wati kumayambiliro a chaka chino iye ananenera za ziwawa zomwe zachitika ku Limbe mu mzinda wa Blantyre ndipo wapempha anthu kuti apemphererebe dziko lino kwambiri.

Malingana ndi mneneri Mtupa, kumayambiliro kwa chakachi Mulungu anamuuza kuti achenjeze dziko lino kudzera mu uneneri oti m’dziko muno mukhala mukuchitika zipolowe.

Mukunenera kwake, Mtupa anafotokoza kuti anthu ambiri m’dziko muno adzafika potopa ndizochitika za akuluakulu a boma ndipo ananena kuti tsiku lina anthu adzagwirana manja ndikuyamba kugenda akuluakulu a bomawo.

“Kuzakhala kuukira kwa anthu; ndipo m’maso anga auzimu ndikuwona gulu la anthu litagwirana manja kumagenda anthu a boma, izi zichitika ndithu, ofunika tipempherere dziko la Malawi kwambiri,” anatero mneneri Mtupa mu ulosi wake kumayambiliro a chaka chino.

Mneneri Mtupa wati uneneriwu wakwaniritsidwa potsatira zipolowe zomwe zinachitika mu msika wa Limbe ku Blantyre komwe anthu okwiya anagenda akuluakulu a khonsolo ya Blantyre.

Munthu wa Mulunguyu wati zomwe zachitikazi ndi ndendende zomwe Yehova anamuuza kuti zichitika ndipo kudzera pa tsamba lake la fesibuku walimbikitsa a Malawi kuti apitilize kupempherera dziko lino kwambiri.

Pakadali pano Mtupa wabweleza kukumbutsa anthu m’dziko muno zakufunika komaika chidwi pa mauneneri omwe amapelekedwa ku dziko lino ndi azitumiki a Mulungu osiyanasiyana.

Iye wati Mulungu amapeleka mauneneriwa pofuna kuchenjeza zomwe zidzachitike ku tsogolo zomwe wati zimatheka kusinthika ndi pemphero lokha basi.

Lachiwiri pa 21 November, 2023, kunali chipwilikiti ku Limbe pomwe ochita malonda mu mphepete mwa misewu anagenda akuluakulu ochokera ku khonsolo ya Blantyre omwe anapita kukawachotsa m’malo osaloledwa omwe amachitira malonda gawo.

Zinthu zinafika pothina kwambiri pomwe apolisi anathira utsi othetsa misozi pofuna kubweretsa bata, zomwe zinapangitsa kuti bata lisokonekere ndipo mashopu ambiri anatsekedwa.

Advertisement