Choipa chitsata mwini: sitima yanyenya mwendo wa ofuna kuba mafuta

Advertisement

Mnyamata wina wa zaka 18 ku Balaka ali mu ululu owopsa pomwe wanyenyedwa mwendo ndi sitima yomwe anaidumphira ikuyenda kuti akabemo mafuta.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Balaka a Gladson M’bumpha, ovulazidwayu wazindikilidwa ngati a Lawrence Yakobe omwe akumana ndi zakudazi lachitatu pa 22 November, 2023.

A M’bumpha ati Yakobe anadumphira sitima ya pa mtunda yomwe imachokera ku Moatize m’dziko la Mozambique kuti akabemo dizilo.

Apolisiwa ati sitimayi itafika pa mlatho wa Mkaya m’boma la Balaka, tsizinamtoleyu anayang’anayang’ana m’malo onse osungira mafuta musitimayi koma sanapeze olo dontho.

Zitatele mkuluyu anaganiza zodumphamo musitimamo kuopa kungamuchele koma anakadziwa sakanapanga chibwana chamchombo lendechi kamba koti anakanika kudumpha bwino bwino.

“Pamenepo, a Yakobe adaganiza zodumpha m’sitimayo koma mwatsoka adagwa pansi ndi kupondedwa ndi sitimayo.

“Mlonda wogwira ntchito Ku kampani ya njanje ndi amene adawapeza a Yakobe ndipo iye adadziwitsa akuluakulu a ku siteshoni ya Mkaya omwe adapita nawo kuchipatala chachikulu cha boma la Balaka,” anatelo a M’bumpha.

M’bumpha wati kamba koti mwendo wa mazere wa Yakobe unanyenyeka kwambiri, madotolo pa chipatala cha Balaka awudula ndipo mkuluyu akulandirabe thandizo la mankhwala.

A Yakobe, amachokera m’mudzi wa Mkaya, mfumu yaikulu Mkaya Ku Balaka komweko ndipo akuyembekezeka kukayankha mlandu wofuna kuba zinthu akatulutsidwa m’chipatala.

Advertisement