Chiyembekezo cha a Malawi chikhale mwa a Chilima  – atero a Kaliati

Advertisement
Patricia Kaliati is a Malaiw politician who has previously served as a cabinet minister

Patricia Kaliati yemwe ndi mlembi wamkulu wa chipani cha UTM wauza a Malawi kuti akuyenera kuyika maso komanso chiyembekezo pa a Saulos Chilima yemwe ndi mtsogoleri wachipanichi.

A Kaliati amayankhula izi dzulo m’boma la Kasungu pamwambo olandira mamembala okwana 79 omwe ali adindo  komanso anthu ena osiyanasiyana ochokera mzipani monga za AFORD, MCP ndi DPP. 

A Kesamula Kaning’a omwe anali Gavanala wa chipani cha AFORD mchigawo chapakati anayankhulapo pa mwambowu ndipo m’kunena kwawo anati chifukwa chimodzi chawapangitsa kupita ku UTM ndichakuti chipani cha AFORD chilibe tsogolo ndipo iwo apita ku UTM kamba kakuti chipanichi chili ndi tsogolo.

Poyankhulanso, a Kaliati anapitiliza kunena kuti chipani chawo sichambumba koma ndi cha anthu. Iwo anatinso ngati chipani akuyembekezereka anthu ochuluka kuchoka ku zipani zina ndikulowa mchipanichi ndi cholinga chofuna kugwilira ntchito limodzi.

Iwo anapitilizanso kufotokoza kuti mwambowu siwukutanthauza kugawana zida kwa Tonse Alliance koma kuti iwo akuchita izi ponena kuti aliyese akukweza mzere wake.

Anthu omwe alowa mchipani cha UTM wa apemphedwa ndikulimbikitsidwa kuti apilize kugwira bwino ntchito zawo ngati momwe anali kuchitira ali kuzipani zinazi.

Wolemba: Ben Bongololo Gondwe

Advertisement