Mai Mbambande yapepesa: Yaletsa anthu kusonkha ndalama yokabweza kwa mayi Mpinganjira

Advertisement
Deborah Mbale is a Malawian woman who runs a an elderly home called Mai Mbambande

Bungwe la Mai Mbambande motsogozedwa ndi Deborah Mbale, lapepesa mkazi wa mpondamatiki Thom Mpinganjira, mayi Triephornia kamba kosabwera poyera ndi kunena kuti mkazi okwatiwa mkumbuyo komweyu anapeleka 2.5 miliyoni kwacha pa nthawi yomwe bungweli limapemphetsa ndalama.

Mayi Mpinganjira anabwera poyera ndikudzudzula utsogoleri wa bungwe la Mai Mbambande kamba kopitiliza kupemphetsabe ndalama yokwana K800,000 pomwe iwo anathandiza bungweli ndi ndalama yokwana 2.5 miliyoni kwacha komaso kuti bungweli silinabwere poyera ndikuthokoza za ndalamayi.

Koma podziikira kumbuyo, mkulu wa Mai Mbambande Deborah Mbale anati kusabwera poyera ndikuthokozaku ndi kamba koti bungweli silimadziwa kuti ndalamayi watumiza ndi ndani ndipo anati bungweli limapitilizabe kupemphetsa ndalama yokwana K800,000 kamba koti zofuna ndalama ku bungweli ndi zambiri.

Koma pomwe mtsutso Unafika pa mpondachimera pa masamba a nchezo pa zayemwe analakwitsa pa anthu awiriwa, Mai Mbambande abwera poyera ndikupepesa mayi Mpinganjira pa zomwe bungweli linachita zosathokoza kapena kufotokoza pa mbalambanda kuti mayiwa anapeleka ndalamayi.

“Monga Mai Mbambande Foundation, ndife odzipereka kulimbikitsa ndi kupititsa patsogolo moyo wa okalamba. Timakhulupilira kumasuka ndi kuchita zinthu poyera ndipo timakhala ndi miyezo yapamwamba muzochita zathu zonse. Posachedwapa, mayi Mpinganjira adapereka ndalama zokwana K2,500,000 ku ntchito yathu. Komabe, panali kusamvana komwe kwadzetsa chisokonezo.

“Tikuwapepesa mayi Mpinganjira chifukwa chosabwera poyera ndi kunena za thandizo lawo lomwe anatipatsa monga momwe timachitira. Pokumbukira kuti iyi inali nthawi yoyesa kwa ife, tikuvomereza pakulephera kwathu. Tikufunanso kupepesa kwa anthu onse chifukwa cha chisokonezo chomwe nkhaniyi yabweretsa. Pambuyo pa zonse, tili ndi okalamba osalakwa omwe akudalira ife,” wapepesa Mai Mbambande muuthenga omwe walembedwa mchizungu.

Bungweli lati potsatira chipwilikiti cha nkhaniyi makamaka pa masamba a nchezo, akuluakulu a bungweli anakumana nchipinda chomata ndi mai Mpinganjira ndipo akambirana zomwe zidachitika kuti bungweli lilephere kubwera poyera ndikukamba za ndalama ikunenedwayi komaso lawafotokozera momwe ndalama yawo inagwilitsidwira ntchito.

Bungweli lapemphaso anthu omwe ayambitsa gulupu la ‘WhatsApp’ komwe a kuti anthu akusonkherana ndalama yokwana 2.5 miliyoni kwacha yoti ikabwezedwe kwa mai Mpinganjira kamba kofuna kuthokozedwa poyera atapeleka thandizo ku bungweli kuti asatelo ponena kuti uku sikukhala.

“Tadziwitsidwa za gulu lomwe likutolera ndalama kuti libweze kwa mayi Mpinganjira. Tikukupemphani kuti musagwiritse ntchito njira imeneyi. Timayamikira chikondi chimene mukupitiriza kutisonyeza, koma tikupempha mokoma mtima kuti tisaponye miyala kapena kuchita mopwetekedwa mitima. Tisasiye kuyang’ana chitsogolo ndipo m’malo mwake tigwiritse ntchito ndalama zimenezi kupititsa patsogolo zolinga zathu,” wateloso Mai Mbambande.

Bungweli lathokozaso mai Mpinganjira ndi onse amene akupitiriza kuwapatsa thandizo losiyanasiyana ndipo lalonjeza kupitilizabe kukonza zolephera zawo ponena kuti zomwe za chitikazi zawapatsa phunziro.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.