Mwamva kulira kwa a Malawi bwana – HRDC yayamikira Chakwera

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Bungwe lomenyera ufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) layamikira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera poyankhula zomwe akuti zikusonyeza kumva kulira kwa a Malawi, ndipo HRDC yati uwu ndi utsogoleri omwe a Malawi amawufuna.

Potsatira kuchepa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha sabata yatha,  lachitatu madzulo a Chakwera anayankhula ku mtundu wa Malawi ndipo mwa zina alengeza mfundo zofuna kuchepetsa ululu kamba ka kuchepa mphamvu kwa ndalama ya dziko lino.

A Chakwera ati kuyambira pano mpaka kufika kumathero kwa chaka chino, iye komaso akuluakulu onse a boma sakhala ndi maulendo opita mayiko akunja zomwe akuti zithandizira kupulumutsa ndalama za misonkho ya a Malawi.

Kupatula apo, mtsogoleriyu walamulaso kuti malipiro a anthu ogwira ntchito m’boma akuyenera akwezedwe komaso anatsindika za mfundo yokweza malipilo oyambira pa ntchito  kungotchulapo zochepa chabe.

Anthu ena omwe anayikira ndemanga pa tsamba lathu la fesibuku komaso m’masamba a nchezo osiyanasiyana pa za zomwe anayankhula a Chakwera-zi, awonetsa kukhutira ndi zomwe zanenedwazi pomwe ena ati pali zinthu zina zomwe mtsogoleri wa dzikoyu amayenera kufotokoza bwino.

Munthu wina anapeleka chitsanzo cha nkhani yochepetsa maulendo akunja ponena kuti a Chakwera amayenera kufotokoza kuti ndimaulendo a ngati omwe amayenera kuyenda omwe ayimitsidwa komaso kupeleka mndandanda wa akuluakulu a boma omwe ali kunja omwe walamura kuti abwelele kuno kumpanje nsanga.

“Lero ndi pa 15 November. Akuyenera anene maulendo omwe amayenera kuyenda kuchoka pano kufika pa 31 December, 2023. Kodi angatchule mayina a nduna zomwe wazilamura kuti zibwere kuno ku mudzi kuchoka kunja komwe zili?” Anatelo munthu wina muuthenga omwe analemba muchizungu.

Ngakhale zili choncho, bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Right Defenders Coalition (HRDC) layamikira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ponena kuti kuyankhula kwake ndichisonyezo choti wamva kulira kwa a Malawi omwe akudandaula potsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha.

Kalata yomwe bungwe la HRDC latulutsa yomwe wasayinira ndi mkulu wake a Gift Trapence, yati mwazina ikukhulupilira kuti mfundo zomwe a Chakwera akhazikitsa zithandiza kuti anthu asakhale pachipsinjo kwambiri ndo kugwa kwa mphamvu kwa ndalama ya dziko linoyi.

“Ife ngati HRDC, tikuyamikira ndi kulandira zomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anena zomwe zikusonyeza kulabadira kulira kwa a Malawi polengeza njira zomwe zingathandize a Malawi kuti asavutike potsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya dziko lino. Uwu ndi utsogoleri omwe a Malawi akhala akuufuna.

“Njira zomwe zaperekedwa ndizokwanira ndipo chofunikira ndikuonetsetsa kuti njira zomwe zaperekedwazi zikutsatilidwa. Timadziwa nthawi zina kuti nzosavuta kunena kuposa kuchita,” yatelo HRDC.

Pakadali pano HRDC yapempha mtsogoleri wa dzikoyu kuti asankhe gulu la anthu loyima palokha kuti liwone ndikutsata ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa zofuna kupulumutsira ndalama za boma ndipo lati gululi likuyenera kumauza a Malawi kuchuluka kwa ndalama zomwe boma likhale likupulumutsa kutsatira ndondomeko zopulumutsira ndalamazi.

Kupatula apo bungweli lati palokha liwonetsetsa kuti ndondomeko zomwe Chakwera wapeleka zikutsatidwa ndi kuti ndalama za boma zikupulutsidwadi.

Advertisement