Ofesi ya zaumoyo m’boma la Zomba yapempha mafumu kuti awonetsetsese kuti anthu awo akhale ndi zimbudzi pofuna kupewa kolera.
Wofalitsa nkhani ku ofesi yadza umoyo Boma la Zomba Arnold Mndalira ndiyemwe wayankhula izi ku Zomba pa msonkhano wa atolankhani omwe adakonza pofuna kudziwitsa olemba nkhani momwe kampeni ya “Tithetse Kolera” ikuyendera m’bomali.
Mndalira adati mamfumu azindikire kuti ali ndi udindo wosamalira anthu choncho ndikofunika kuti azilimbikitsa anthu awo kumwa madzi a ukhondo othira mankhwala a chlorine komanso kusamba m’manja ndi sopo panthawi yomwe abwera kuchokera kuchimbudzi.
Iye adapemphanso mamfumu kuti alangize anthu m’madera mwao kuti munyengo ino ya mvula anthu asamaphike zokudya pamikumano monga pa maukwati, zinkhoswe komanso pamaliro kuti apewe matenda a Kolera.
Pamenepa ofesi ya zaumoyo idati ogwira ntchito za umoyo komanso ogwira ntchito modzipereka akhala akuyenda khomo ndi khomo kupereka ma uthenga kwa anthu amomwe angadzitetezere kumatenda a kolera ndipo akuyembekedzera kufikira midzi yokwana 1,100.
“Ife a zaumoyo m’boma lino la Zomba tikupempha kuti tigwirane manja kuti tilimbane ndi matenda akolera ndipo aliyense adziwe kuti kupewa matendawa ndi kwa munthu wina aliyense osati Boma lokha kapena atolankhani,” adatero Mndalira.
Ofesi ya zaumoyo ku Zomba ikugwira ntchito ya Tithetse Kolera ndithandidzo lochokera ku Bungwe la UNECEF ndipo ndi zokwana 91.5 million kwacha.
Mu boma la Zomba, anthu anayi (4) ndi omwe agwidwa ndi matenda akolera kuyambira mwezi wa October ndipo anthuwa ndiwochokera mdera la Matawale, mmudzi mwa Mulosola, Namadidi komanso Sadzi.