Amangidwa chifukwa chofuna kugulitsa mimba ku Nkhotakota

Advertisement
Malawi24.com

A Polisi m’boma la Nkhotakota amanga a Frank Malaki a zaka 23 ndi mkazi wawo Enita Joseph chifukwa chofuna kugulitsa  mimba pa mtengo wa K200,000.

Awiriwa amafuna kugulitsa mimba ya a Joseph kwa munthu wina ochita malonda ku Nkhotakota komweko.

Malingana ndi mneneri wa Polisi m’bomali a Paul Malimwe, banjali pa 7 Novembala chaka chino linapita kwa munthu wina ochita malonda ku Nkaika m’bomalo ndipo anamuuza kuti iwowo ndi okonzeka kuchotsa mimbayo ndikuyigulitsa pa mtengo wa K200,000.

Iwo amafuna ndalamayi kuti akabwezela ngongole ya banki mkhonde.

Atamva izi, mkulu ochita malondayo anakanena ku Polisi ya Mkaika ndipo apolisi amanga banjali.

Advertisement