Aphunzitsi apatsidwa ng’ombe kamba kokhonzetsa bwino ana

Advertisement
Malawi teachers appreciated by their former students

Nzako akati konzu naweso umati konzu. Uwu ndi mwambi omwe makolo a ophunzira pa sukulu ya sekondale ya Karonga Girls agwiritsa ntchito popeleka mphatso ya ng’ombe kwa aphunzitsi kamba kokhozetsa bwino nayeso a JCE komaso MSCE chaka chino.

Sukulu ya atsikana ya Karonga inakhozetsa ana onse pa mayeso a Junior Certificate of Education (JCE) chaka chino kuyimilira 100 pelesenti (percent) ndipo mayeso a Malawi School Certificate of Education (MSCE) ana olephera sanapitilire asanu zomwe zimayimilira 97 pelesenti.

Podziwa kuti kulimbikira kumalipira, makolo a ana omwe amaphunzira pa sukuluyi, anachita limodzilimodzi ndikuwagulira aphunzitsiwa mphatso yamtengo wa pamwamba, ng’ombe yoti onse agawane.

Malingana ndi wapampando wa bungwe la makolo ndi aphunzitsi pa sukuluyi William Matchona Ngwira, wati makolowa anachita nsonkhensonkhe ndipo anakwanitsa kugula ng’ombe pantengo wa K550, 000 yomwe akayipelela kwa aphunzitsi pa sukulupo.

A Matchona Ngwira anauza nyumba ina yofalitsa nkhani m’dziko muno kuti kupereka ng’ombe-ko kwachitika ndicholinga chofuna kuyamikira aphunzitsiwo chifukwa chochita bwino pamayeso onse a JCE komaso MSCE.

Iwo anati ali ndi chikhulupiliro kuti zomwe achitazi, ziwapatsa mangolomera aphunzitsiwa kuti apitilile kulimbikira pa ntchito yosula ana pa sukuluyi ndicholinga choti zotsatira zabwino pa mayeso onse aboma chikhale chizolowezi.

Polandira mphatso-yi, m’phunzitsi wamkulu pasukuluyi, Chimwemwe Mithi, adathokoza makolowo chifukwa cha mphatsoyi ndipo anatsindika kuti aphunzitsi pa sukulu ya atsikana ya Karonga akusimba lokoma kamba ka kulimbikira kwawo.

Iwo anati zomwe achita makolozi ndizochititsa kaso komaso chisonyezo choti makolowa amawaganizira ndi kuwayamikira pa ntchito yabwino yomwe amagwira yochotsa umbuli aja awo ndipo ati izi zilimbikitsa aphunzitsiwa kudzipeleka mwa mnanu.

Mayi Mithi analonjeza makolowa kuti sukulu-yi ipitiliza kulimbikitsa ophunzira kukhala osunga mwambo, olimbikira komanso kuwayesa mosalekeza kuti nthawi zonse sukuluyi izipeza zotsatira zabwino pa mayeso onse aboma omwe akubwera kutsogoloku.

M’phunzitsi wa mkuluyi anadandulapo za kusowa kwa kalasi yochitira maphunziro a sayasi (laboratory) komanso holo yochitira zinthu zambiri pasukuluyi ponena kuti izi zikusokoneza maphunziro apamwamba kusukuluyi.

Advertisement