Bus ya Mzuni yachita ngozi lero

Advertisement
Mzuzu University students have been involved in an accident on their way to Nkhata Bay on November 4, 2023

Bus ya pa Mzuzu University yomwe nambala yake ndi  MZ10315 yachita ngozi pa Kanduli m’mawa uno pamene ophunzira a sukulu ya ukachenjedeyi anali pa ulendo opita m’boma la Nkhata-Bay.

M’modzi mwa ophunzira amene anali nawo pa ulendowu  anauza Malawi24 kuti zikuonetsa kuti ngoziyi yachitika kamba kakuti Bus yo inaduka mabuleki.

Pakadali pano omwe avulala athamangira nawo kuchipatala cha Mzuzu Central Hospital.

Ophunzira a zophikaphika komanso zoyendetsa nyumba zogona alendo omwe ali muchaka cha nambala 4 anali pa ulendo wa maphunziro omwe lero amapita m’boma la Nkhata-bay.

Wolemba: Ben Bongololo, Mzuzu

Advertisement