Kulibe mphenzi yogulitsa – atero azanyengo

Advertisement
Charles Vanya Malawi

Nthambi yowona zanyengo yatsutsa mphekesera zomwe zimamveka kuti anthu ena amatha kulenga mphenzi m’matsenga ndipo ena amagula pa mtengo wa 30 kapena 50 kwacha kuti aphe anzawo mwamatsenga.

Izi zadziwika pamene nthambiyo inali ndi nkumano ndi atolankhani olemba nkhani za nyengo kuchokera muzigawo komanso mawailesi ndi kanema owulusa mau osiyanasiyana omwe unachitikira ku Liwonde m’boma la Machinga.

Wachiwiri kwa wamkulu wa  zanyengo a Charles Vanya anati nthawi ya dzinja ziopsezo komanso  zobwera chifukwa cha mphenzi ndi mvula ya mkuntho zimachuluka.

Iwo anati mphezi imapangika pamene dera latentha kwambiri komanso chinyontho chachoka pansi nkukwera m’mwamba zomwe zimapangitsa kuti chinyontho chizizire nkuyamba kuwundana kenaka kupanga madontho amadzi omwenso akazizira kwambiri amapangano timichenga tonga madzi owuma omwe pachizungu amati Ice omwe akagwa amatchulidwa kuti matalala.

Adaonjezera kuti zimenezi zimachitika m’mwamba chifukwa chowombanawombana  ndipo zimapangitsa kuti pansi pakhale kuti papanga nyesi chifukwa pamakhala kuti papangidwa tchaji muja achitira magetsi ndiye nyesi ikachuluka kwambiri pamakhala kuti papanga nyesi yomwe imafunika kuti ithesedwe mphamvu.

“Ndiye chilengedwe cha Mulungu anapanga kuti ngati pansi pa mtambo papanga nyesi ndiyekuti pansi panthaka pamayenera papange nyesi yotsutsana ndi inzake muchizungu amati positive ndi negative ndiye zimenezi zikamachitika nyezi ija imafuna njira yoti idzerepo yomwe anthu komanso zomera pansi amayipatsa.

“Chifukwa chake ngati nthambi yazanyengo timalangiza anthu kuti asakhale pafupi ndi mtengo, asayende pamene mvula ya mphedzi ikugwa chifukwa pakutero munthu amakhara chinthu chachitalii choti mphenzi itsikirepo. Komanso tikupempha kuti  anthu apewe kukhala onyowa pamene mvula ikugwa ngati munthu amasamba akuyenera kukhala pamalo owuma mpakana mvula ija ithe chifukwa mphezi imadutsira mwa munthu yemwenso wanyowa. Tilekenso mchitidwe oseweretsa zipangidzo zomwe timagwiritsira magesi ngati lamya,” a Vanya adatero.

Iwo adawonjezera ponena kuti pamene mphenzi ikugwa nthawi yoti munthu akuchokera ku munda ndibwino kugwada mosagunditsa mawondo komanso manja pansi kuchita ngati mowerema kuti mphenzi itsakukhudze chifukwa mpweya onse ozungurira umakhala kuti wagwira nyesi yamphedzi ija.

A Vanya anatinso  nthambiyi itawona kuti ikufunika kuti idzigwira ntchito mwadongosolo komanso mwa malamuLo omwe angamawapatse mphamvu pantchito yawo, awona kuti afunika akhale ndi malamulo omwe mu chizungu amati bill omwe angamatsatire chifukwa zinthu ngati nyumba komanso misewu zikuyenera kumangidwa motsatira nyengo.

Poyankhulapo, mkulu wa bungwe la atolankhani olemba nkhani zanyengo la Network of Journalists on  Climate  (NJC) Deitrich  Frederich  analimbikitsa  atolankhaniwa kuti nkhani  komanso mapologalamu omwe amawulutsa akuyenera kukhala okhunzana ndi zanyengo.

Kutsatira mvula yomwe inagwa sabata lathu, anthu awiri ndi omwe anamwalira komanso  ena anayi anavulala kamba ka mphezi yomwe inachitika mu M’boma la Kasungu.

Advertisement