A Malawi awukira bungwe loyendetsa mpira wa miyendo m’dziko muno la Football Association of Malawi (FAM), ponena kuti K1 miliyoni yomwe yati ipeleka kwa osewera aliyese wa Scorchers kaamba kopambana chikho cha Cosafa ndiyochepa kwambiri.
Lolemba bungwe FAM linalengeza kuti kupatula ndalama zomwe osewera akuyenera kulandira popamba masewero (game bonus), liperekaso ndalama yokwana 1 miliyoni kwacha kwa osewera aliyense wa Scorchers.
Mtsogoleri wa FAM a Walter Nyamilandu Manda, anayankhula izi pamwambo wamgonero omwe unachitika muzinda wa Blantyre pokondwelera kuti timu ya mpira wamiyendo ya atsikanayi yapambana chikho cha Cosafa Women.
A Nyamilandu Manda anati atsikanawa achotsa manyazi dziko lino kotelo kuti K1 miliyoni ndichithokozo pa chipambano cha timu ya Scorchers.
Koma pomwe bungwe la FAM limawona ngati lapanga chithu cha mtengo wapatali, a Malawi ochuluka ati ndalama ya chithokozoyi yachepa kwambiri.
Anthu ena omwe anaikira ndemanga za nkhaniyi pa tsamba lathu la fesibuku, ati potengera momwe atsikanawa anadzipelekera komaso potengera m’mene nkhani za chuma zikuyendera m’dziko muno, ndalamayi akuyenera atayiwonjezera.
“A Walter Nyamilandu-Manda, apatseni asungwana a Scorchers MK20 million aliyense agule maplot mtown umu. Nanga mmene asewelera atsikana muja kupambana game yiliyonse nkutenga chikho basi alandire MK1 million? Pali Yesu? A Nyamilandu Manda ndinu amene mukuwononga tsogolo lampira mdziko muno.
“Inuyo mmayendera vimagalimoto vopuma vodula, ma allowance mbwe mbwe koma eni ntchito zero. Musawapatse MK1 million ana, ndalama ndizawo, apatseni agawane. Olo Atati agawane ma MK30 million, kutsalanso chenje,” watelo munthu wina pa fesibuku.
Munthu winaso wauza mtsogoleri wa FAM a Nyamilandu Manda kuti awaganizile atsikanawa powonjezera ndalama yomwe apatsidweyi.
“Inu one million kwacha ndi chani?? Equivalent to the cost of living now it’s like (Kutengera ndi m’memne zinthu zilili pano zili ngati) mwawapatsa ya chiwayatu. Uzitolele Walter Nyamirandu,” wateloso munthu wina.
Ngakhale zili choncho, anthu ena ati ndalamayi ndiyokwana potengera kuti time yomwe yapambana chikho cha Cosafa Women siyimapatsidwa ndalama ina iliyose kupatula kupatsidwa chikho.
Timu ya Scorchers yatenga chikho cha Cosafa Women itapambana masewero ake onse asanu ndipo inagoletsa zigoli zokwana khumi mphamvu zisanu ndi zinayi (19).