Nanga Ayra Starr simukumunena bwa? Queen Sheba adandaula zakutozedwa pa mavalidwe ake

Advertisement
Ayra Starr is a Nigerian Musician with over a million followers on social media. Her songs include Rush and Sability

Oyimba Racheal Muyepa yemwe amadziwika kwambiri ndi dzina loti Queen Sheba wati ndiodabwa kuti a Malawi sakuyankhula kanthu za mavalidwe a oyimba wa ku Nigeria Ayra Starr yemwe anali m’dziko muno, ponena kuti anakakhala iye kunakakhala maphuzo.

Oyimba amene wabhebha kwambiri m’dziko la Nigeria pano, Oyinkansola Sarah Aderibigbe yemwe amatchuka ndi dzina loti Ayra Starr, anali m’dziko muno paphwando la maimbidwe ku Lilongwe.

Ayra Starr anali oyimba olemekezeka pamene Kelly Kay amasangala kuti watha zaka khumi (10) chiyambileni kuyimba ndipo phwandoli linachitikira pa bwalo la zamasewero la Bingu lamulungu pa 15 October, 2023.

Ayra Starr is a Nigerian Musician with over a million followers on social media. Her songs include Rush and Sability
Ayra Starr anavala chonchi pamene amaimba ku Malawi (Wojambula: https://twitter.com/Chinosssssssss)

Oyimba wa m’dziko la Nigeria-yu anavala mosinira kwambiri kotelo kuti mbali yochuluka ya thupi lake inali pa mbalambanda, osaphimbidwa kose.

Ngakhale zili choncho, a Malawi sanayankhule motsutsana ndi kavalidweka zomwe zadandaulitsa oyimba Queen Sheba yemwe akuti amayembekeza kuti anthu adzudzula mavalidwe a Ayra Starr.

Muuthenga wake omwe anaulemba pa tsamba lake la fesibuku, Sheba wati ndiwodabwa kwambiri kuti a Malawi akhala chete pamene anakakhala iye kunakhala kusambwadzidwa ndi maphuzo.

“Izizi kuvala munthu waku malawi ndi hule komaso ngosalongosoka. Awawa avaya zovala za mahule akumalawi kuli ziiiii palibe akuyakhula za dressing yake. Ine mkangovala kuchita kusowa mtendere ndikutozedwa. Wina dzamutukwana,” watelo Queen Sheba pa fesibuku.

Pakadali pano anthu akupeleka ndemanga zosiyanasiyana pa zamowe mwayankhula Queen Sheba; pomwe ena akugwirizana naye ndipo ena akutsutsana naye.

Advertisement