Nayonso Premier Bet yazituluka – ati chuma sichikuyenda, ma agent ntchito yatha basi

Advertisement
Sports Betting Malawi

Kapena mwina a Malawi tasukutsula mmaso pa njuga mpaka takhaulitsa mzungu? Koma a kampani ya Premier Bet ati vuto ndi chuma. Ndipo tsopano ayamba kutuluka msika wa ku Malawi. Awo paulendo kutsatira DSTV.

Kampani yotchuka pa njuga ya Premier Bet yalengeza kuti ikutseka malo onse amene anthu amakakungira ma tikiti a njuga. Malinga ndi chikalata chimene kampaniyi yatulutsa chat kuyambila pa 30 Sepitembala sakufuna kuonanso agent aliyense akupanga za iwo.

“Sitikupanga phindu, pachuluka kampani za njuga ndipo zonsezi kuphatikizapo ndi kusokonekera kwa chuma mu dziko muno ndiye bola kungozisiya,” chatero chikalatachi.

Kampaniyi yachenjeza onse amene amachita u agent nawo kuti akuyenera akabwenze zipangizo kuyambira pa 3 Okotoba ndipo iwo aonetsetsa kuti athana ndi ngongole zonse za omwe akhala akupambana.

Kampani ya Premier Bet ndi imene inautsa mudyo mwa a Malawi pa nkhani za njuga za masewero a mpira. Ngakhale kuti anthu ena akhala akuchita mphumi ndi kuphula ma miliyoni kuchoka ku kampaniyi, anthu ena akhala akukhaula nayo ena mpaka anafika pozipha ataluza ku njuga.

Chiganizo cha kampaniyi chabwera pamene kampani youlutsa Mawu ya DSTV nayo inanyanyala pa mkangano ndi bungwe la MACRA.

Advertisement