Boma lauza apolisi kuti amange anthu omwe anazula mipando ku Bingu

Advertisement
Bingu Stadium chairs which were damaged by football fans

Nduna ya zamasewero Uchizi Mkandawire yapempha apolisi kuti afufuze anthu omwe awononga mipando yoposa 200 ku bwalo la zamasewero la Bingu ku Lilongwe

A Mkandawire ayankhula izi atayendera bwalo la zamasewero la Bingu komwe anthu anazula mipando 239 pomwe anakaonela mpira wa pakati pa Silver Strikers ndi Mighty Wanderers.

Iwo anati apolisi agwire ntchito yawo pomanga omwe awononga mipandoyi.

“Izi ndi zomvetsa chisoni kwambiri, zititengera ndalama zochuluka kulikonzanso bwaloli kuti alivomereze a CAF. Kuphatikiza apo ndalama zomwe tinamangira bwalo la zamaseweroli ndi zangongole zomwe sitinamalize kubweza,” anatero a Mkandawire poyankhula ndi wayilesi ya MBC.

Loweruka lathali, pa bwalo la Bingu panali masewera apakati pa Mighty Wanderers ndi Silver Strikers mu chikho cha Airtel.

Komalizila kwa masewerawa, Silver inagoletsa chigoli koma osewera a Wanderers anadandula kuti oyimbira mpira anali ataimitsa kale mpira. Chigolichi chinapangitsa kuti mpira uthere panjira ndipo anthu ena anatengerapo mwayi powononga mipando yomwe amakhalila anthu akamawoners mpira.

Advertisement