UDF ndi UTM zati MCP yapereka ndalama ndi ufa kwa anthu odzaponya voti

Advertisement
Malawi Congress Party supporters leave a rally carrying maize flour

Zipani za United Democratic Front (UDF) ndi UTM zadandaula kuti chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chimapereka thumba la ufa lolemera 25 kilogalamu komanso ndalama kwa anthu omwe aponye voti pachisankho chachibwereza pa 26 September chosankha khansala ku Ntiya Ward mu Mzinda wa Zomba zomwe akuti ndizoletsedwa pamalamulo achisankho.

Mlembi wamkulu wachipani cha UDF Abubaker M’baya komanso membala wachipani cha UTM yemwenso ndi Phungu wa Zomba Changalume a Biziweck Million ndiwomwe ayankhula izi ndi Malawi24 ndipo ati akapereka madandaulo awo ku Bungwe lowoona zachisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) zankhaniyi.

Iwo atinso kupatula kupereka ufa ndi ndalama kwa anthu ovota pachisankhochi, nduna za boma zitatu Loweruka zidagwiritsa zipangizo za boma monga galimoto ndi owateteza a Police zomwenso adati ndiidzosemphana ndi malamulo achisankho.

Lowereka, chipani cha MCP pa msonkhano wake wokopa anthu kuti adzavotere Khansala wachipani chawo ku Ntiya Ward mu Mzinda wa Zomba, chidali kupereka thumba limodzi la ufa lolemera 25 kilogalamu komanso ndalama kwa anthu odzaponya voti ndipo anthuwa asadawapatse thumbalo amayamba awonetsa chiphatso chawo chovotera.

Atolankhani amaletsedwa kujambula zithunzi ndipo mtolankhani wina adamuuza kuti afute zithunzi zomwe adajambula komanso amafuna kumuswera kamera yake.

Tinayesa kuti tiyankhule ndi wofalitsa nkhani za Bungwe la MEC Samgwani Mwafulirwa koma lamya yake ya mmanja simapedzeka.

Anthu a ku Ntiya Ward ayamba kuponya voti lero mu chisankho cha chibwereza.

Advertisement